Pitani ku nkhani yake

Anthu Akupatsidwa Mabaibulo a M’zinenero Zawo

Anthu Akupatsidwa Mabaibulo a M’zinenero Zawo

A Mboni za Yehova akupereka Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika kwa munthu aliyense amene angafune kuliwerenga.

Ngakhale kuti makampani osindikiza Mabaibulo asindikiza Mabaibulo mamiliyoni ambiri a m’zinenero zosiyanasiyana, anthu ambiri amalephera kupeza Mabaibulo. Izi zimachitika chifukwa cha umphawi komanso atsogoleri a zipembedzo ena safuna kuti anthu awo akhale ndi Baibulo la m’chinenero chawo. Komabe, a Mboni za Yehova amapereka Baibulo la Dziko Latsopano m’zinenero zoposa 115.

Taonani zitsanzo zotsatirazi:

 • Rwanda: A Silvestre ndi akazi awo a Venantie, omwe ali ndi ana 4, ananena kuti: “Ife ndi osauka kwambiri choncho sitikanatha kugulira munthu aliyense wa m’banja lathu Baibulo lake. Tsopano aliyense ali ndi Baibulo la Dziko Latsopano m’chinenero cha Kinyarwanda ndipo timawerenga Baibuloli pamodzi tsiku lililonse.”

  M’busa wina wa tchalitchi cha Angilikani m’dziko lomwelo ananena kuti: “Baibulo ili ndikulimvetsa kwambiri. Ndilosavuta kumvetsa poyerekezera ndi Mabaibulo onse amene ndinawerengapo. A Mboni za Yehova amafunadi kuthandiza anthu.”

 • Democratic Republic of the Congo: Matchalitchi ena amakana kugulitsa Mabaibulo a m’Chilingala kwa Mboni za Yehova. Chinenerochi ndi chimodzi mwa zinenero zomwe zimalankhulidwa kwambiri m’dzikoli.

  M’pake kuti Baibulo la Dziko Latsopano litangotuluka m’Chilingala, a Mboni za Yehova a ku Congo anachita khama kugwiritsa ntchito Baibuloli komanso kugawira anthu ena. Ndipotu Baibulo la Dziko Latsopano litatuluka m’chinenerochi, anthu anasangalala kwambiri moti apolisi ena amene anali nawo pamsonkhano umene panatulutsidwa Baibuloli, anakhala nawo pamzere kuti alandire nawo Baibuloli.

 • Fiji: Mabaibulo a m’chinenero cha Chifiji ndi okwera mtengo kwambiri moti m’mbuyomu anthu ambiri a Mboni za Yehova ankagwiritsa ntchito Baibulo la Dziko Latsopano lachingelezi. Komabe m’chaka cha 2009, anthu a ku Fiji analandira Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu (Chipangano Chatsopano) m’chinenero chawo.

  Bambo wina anachita chidwi kwambiri ndi Baibulo la Dziko Latsopano la m’Chifiji lomwe linali losavuta kumva moti anapempha wa Mboni kuti amupezere lake. Koma wa Mboniyo anauza bamboyo kuti adikirire kwa mwezi wathunthu kuti Mabaibulowo abwere. Popeza amalifuna mwamsanga, bamboyo analola kuti akakumane ndi munthu wa Mboni wina yemwe anali nalo. Bamboyo analolera kuyenda mtunda wa makilomita 35 kuchokera kwawo kuti akapeze Baibulo la Dziko Latsopano. Atapeza Baibulolo, bamboyo anati: “Baibulo ili ndi labwino poyerekezera ndi Mabaibulo amene timagwiritsira ntchito. Ndi losavuta kuwerenga komanso kumva.”

 • Malawi: Davide atayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova, anthu amene ankapemphera nawo kutchalitchi cha Baptist anapita kunyumba kwake n’kukalanda Baibulo limene anamupatsa. Choncho Davide anasangalala kwambiri atalandira Baibulo la Dziko Latsopano m’Chichewa.

  Atalandidwa Baibulo ndi anthu a kutchalitchi chake, Davide sankadziwa kuti apeza bwanji Baibulo lina chifukwa ku Malawi Mabaibulo ndi okwera mtengo kwambiri. Koma atapatsidwa Baibulo la Dziko Latsopano ananena kuti: “Panopa ndapeza Baibulo labwino kwambiri kuposa limene anandilanda lija.”

Mbali yoyamba ya Baibulo lachingelezi la Baibulo la Dziko Latsopano itatuluka pamsonkhano umene unachitika ku New York City zaka 60 zapitazo, anthu omwe anali pamsonkhanowo analimbikitsidwa kuti: “Muziwerenga komanso kuphunzira Baibuloli . . . . Mukapatsenso anthu ena.” Kuti akwanitse zimenezi, a Mboni za Yehova asindikiza makope oposa 175 miliyoni a Baibulo la Dziko Latsopano. Ndipotu tsopano mukhoza kuwerenga Baibuloli pa Intaneti m’zinenero zoposa 50.