Pitani ku nkhani yake

Ntchito Yosindikiza Mabuku Ikuthandiza Anthu Padziko Lonse Kuphunzira za Mulungu

Ntchito Yosindikiza Mabuku Ikuthandiza Anthu Padziko Lonse Kuphunzira za Mulungu

Padziko lonse lapansi anthu mamiliyoni ambiri amawerenga mabuku ofalitsidwa ndi a Mboni za Yehova, ndipo ena amawawerenga pa zipangizo zamakono monga mmene inu mukuchitiramu. Koma mwina mungadabwe ndi kuchuluka kwa mabuku amene timasindikiza. Pofika m’chaka cha 2013, mabuku athu anali akusindikizidwa m’zinenero pafupifupi 700 ndipo amafalitsidwa m’mayiko 239.

Chisanafike chaka cha 1920, tinkasindikizitsa mabuku ku makampani osiyanasiyana. Pofika m’chakachi, tinayamba kusindikiza magazini komanso timabuku m’nyumba ina yake yomwe tinkapanga lendi m’dera la Brooklyn ku New York. Kuchokera pa nthawiyo kufika pano, tili ndi makina osindikizira mabuku ku Africa, Asia, Australia, Europe, North America ndi ku South America.

Buku Lathu Lofunika Kwambiri

Buku lofunika kwambiri limene timasindikiza ndi Baibulo. Mu 1942 tinayamba kusindikiza Baibulo lathunthu lachingelezi la King James Version. Kuyambira mu 1961, a Mboni za Yehova amasulira komanso kusindikiza Baibulo lathunthu la Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika. Pofika mu 2013 Mabaibulo oposa 184 miliyoni anali atasindikizidwa m’zinenero 121.

Mabaibulo amene timasindikizawa amakhala olimba kwambiri. Izi zili choncho chifukwa mapepala ake ndi apadera kwambiri ndiponso amamatidwa m’njira yakuti asaonongeke msanga. Ndipo zimenezi zimachititsa kuti Mabaibulowa azionekabe bwino ngakhale atamagwiritsidwa ntchito tsiku lililonse.

Mabuku Ena

Timasindikizanso mabuku ena amene amathandiza anthu kulimvetsa bwino Baibulo. Taonani zimene tinachita mu 2013:

  • Magazini yathu ya Nsanja ya Olonda, yomwe ndi magazini yofalitsidwa kwambiri padziko lonse lapansi, imasindikizidwa m’zinenero zoposa 210. Magazini 45,000,000 a Nsanja ya Olonda amasamba 16, amasindikizidwa mwezi uliwonse.

  • Galamukani!, yomwe ndi magazini inzake ya Nsanja ya Olonda, ndi yachiwiri pa magazini amene amafalitsidwa kwambiri padziko lonse lapansi ndipo imasindikizidwa m’zinenero 99. Mwezi uliwonse, magazini 44,000,000 a Galamukani! amasindikizidwa.

  • Buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lili ndi masamba 224 ndipo la chikuto chofewa. Bukuli linakonzedwa pofuna kuthandiza anthu kumvetsa mfundo zosavuta za m’Baibulo. Kuyambira mu 2005, mabuku oposa 214 miliyoni asindikizidwa m’zinenero zoposa 240.

  • Mverani Mulungu ndi kabuku kamasamba 32, komwe kanakonzedwa kuti kazithandiza anthu amene satha kuwerenga bwinobwino. Kabukuka kamathandiza anthu kumvetsa mfundo zosavuta za choonadi pogwiritsa ntchito zithunzi zokongola ndiponso mawu achidule ofotokozera zithunzi. Timabuku toposa 42 miliyoni tasindikizidwa m’zinenero zoposa 400.

Kuwonjezera pa zimene tatchula pamwambazi, a Mboni za Yehova amasindikizanso zinthu zina zosiyanasiyana monga, mabuku, timabuku ndi timapepala. Mabukuwa amathandiza anthu ofuna kuphunzira Baibulo kuti azitha kufufuza mayankho amafunso okhudzana ndi nkhani za m’Baibulo. Amathandizanso anthu kupirira mavuto okhudza moyo komanso kukhala ndi mabanja osangalala. Mu 2012 makina osindikizira mabuku a Mboni za Yehova anasindikiza magazini 1.3 biliyoni ndiponso mabuku ndi Mabaibulo 80 miliyoni.

Makina amene a Mboni za Yehova amasindikizira mabuku, mu 2012 anasindikiza magazini 1.3 biliyoni ndiponso mabuku ndi Mabaibulo 80 miliyoni.

Malo athu osindikizira mabuku ali ku Beteli, dzina lomwe limatanthauza “Nyumba ya Mulungu.” Anthu amene amabwera ku Beteli kudzaona makina athu osindikizira mabuku, amachita chidwi kuona amuna ndi akazi akugwira ntchito mwakhama. Anthu onsewa, amathera nthawi komanso mphamvu zawo pogwira ntchitoyi. Anthuwa akafika ku Beteli, ambiri amakhala kuti sadziwa chilichonse chokhudza ntchito yosindikiza mabuku. Komabe amaphunzitsidwa mwapadera, ndipo zimenezi zimawathandiza kuti adziwe zinthu zambiri. Mwachitsanzo, sizachilendo kuona achinyamata a zaka za m’ma 20 akudziwa bwino kugwiritsa ntchito makina amakono osindikizira mabuku. Makinawa amatha kusindikiza magazini 200,000 pa ola limodzi.

Kodi Ndalama Zoyendetsera Ntchitoyi Zimachokera Kuti?

Ntchito ya a Mboni za Yehova yomwe ikuchitika padziko lonse, imayendetsedwa ndi ndalama zimene anthu amapereka mwakufuna kwawo. Mu August 1879, m’magazini yachingelezi ya Zion’s Watch Tower, yomwe panopa imatchedwa Nsanja ya Olonda, munali mawu awa: “ ‘Sitikukayikira kuti YEHOVA ndi amene akutsogolera ntchito yofalitsa magazini ino, choncho sitidzapemphetsa kwa anthu kapena kuwachonderera kuti athandize pa ntchito imeneyi.” Ifenso tikugwirizana ndi maganizo amenewa.

Koma, n’chifukwa chiyani timathera nthawi yambiri, mphamvu komanso ndalama zochuluka pa ntchitoyi? Kaya mumawerenga Baibulo komanso mabuku osindikizidwa ndi makina athu, kapena mumakonda kuwawerenga pa webusaiti yathu, cholinga chake n’chakuti akuthandizeni kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu.