Bambo wina wa ku Malaysia ananena mawu otsatirawa pofotokoza zokhudza mavidiyo osiyanasiyana a Khalani Bwenzi la Yehova. Iye anati: “Apa Yehova wayankha zimene makolofe timapempha.”

Mavidiyo a makatuniwa, a Kalebe ndi Sofiya komanso makolo awo, amakonzedwa ndi Mboni za Yehova, ndipo pofika pano mavidiyo osiyanasiyana atulutsidwa. Mavidiyowa akupezeka pa jw.org ndipo amathandiza ana kuphunzira mfundo zothandiza, monga chifukwa chake ayenera kupewa kuba komanso mmene angapempherere kwa Mulungu.

Vidiyo yoyamba pa mavidiyowa yamasuliridwa kale m’zinenero zoposa 131 ndipo ikuthandiza kwambiri ana padziko lonse lapansi.

Anthu Akuwakonda Kwambiri

Mayi wina amene ali ndi ana 5 analemba kuti: “Mlungu wathawu, talandira DVD yakuti Khalani Omvera Kuti Mulandire Madalitso. Koma pofika pano taionera kale nthawi zoposa 50.”

Mtsikana wina wazaka 12 ku England dzina lake Millie, ali ndi mchimwene wake wazaka 15, dzina lake Thomas. Mchimwene wakeyu amadwala matenda enaake a muubongo. Millie analemba kuti: “Thomas ali ndi mavidiyo a Kalebe mukompyuta yake yaing’ono ndipo amaonetsa anzake kusukulu. Iye amakonda nyimbo za m’mavidiyowa ndipo amaziimba bwino kwambiri, moti mlongo winawake atamvetsera, analira chifukwa cha chisangalalo. Mavidiyowa amuthandiza kwambiri mchimwene wangayu kuti azitha kuimba bwinobwino.”

Kamtsikana kena dzina lake Ava, kamene kanati kali ndi zaka 8, miyezi 9 ndi masiku 25, kanalemba kuti: “Kalebe ndi mchemwali wake amaphunzitsa bwino kwambiri ana.”

Kamtsikana kenanso dzina lake Mikaylah, kanalemba kuti: “Ndili ndi zaka 6. Ndikuthokoza kwambiri chifukwa chotulutsa DVD yakuti Khalani Omvera Kuti Mulandire Madalitso. Vidiyoyi inandiphunzitsa kumvera makolo anga ndipo ndikamachita zimenezi Yehova amasangalala.”

Ndi Ophunzitsadi

Munthu wina wachinyamata yemwe si wa Mboni za Yehova ndipo amapanga mavidiyo a makatuni, anaonera vidiyo yosonyeza kuti kuba si kwabwino (Stealing Is Bad), yomwe ili m’gulu la mavidiyo a makatuni opangidwa ndi Mboni za Yehova. Munthuyu anagoma kwabasi, makamaka atadziwa kuti ndi anthu ochepa kwambiri amene anapanga vidiyoyi. Iye anati: “Ndikudziwa anthu amene amagwira ntchito m’masitudiyo akuluakulu komanso ang’onoang’ono. M’masitudiyo onsewa mumakhala ntchito yaikulu zedi. Koma akamaliza kupanga vidiyo ya makatuni, anthu amaionera ndi kuseka kwa maola angapo, ndipo zimathera pomwepo. Koma makatuni anuwa ndi apadera. Akusintha moyo wa ana, kuwaphunzitsa kusiyanitsa zabwino ndi zoipa komanso kuwathandiza kuti azisankha zinthu mwanzeru. Mukamapanga mavidiyowa mumakhala ndi cholinga, ndipo akuthandizadi anthu.”

Nawonso makolo padziko lonse akugwirizana ndi zimene wachinyamatayu ananena. Mwachitsanzo, mayi wina analemba kuti: “Nthawi ina yake, mwana wanga wamwamuna wa zaka zitatu dzina lake Quinn, ankaonera vidiyo yanyimbo yakuti Tikhale pa Ubwenzi ndi Yehova. (Gaining Jehovah’s Friendship) Vidiyoyi ili mkati, anandiyang’ana kenako n’kugwira pachifuwa chake, n’kundiuza kuti: ‘Amayi, ndimasangalala mumtimamu ndikamaonera vidiyoyi.’ ”