Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

Masamba Achepa Koma Zinenero Zachuluka

Masamba Achepa Koma Zinenero Zachuluka

Kuyambira mu January 2013, masamba a magazini iliyonse ya Galamukani! komanso Nsanja ya Olonda yogawira anachepetsedwa kuchoka pa 32 kufika pa 16.

Anthu omasulira mabuku azitha kumasulira magazini m’zinenero zochuluka chifukwa cha kuchepa kwa masamba a magaziniwa. Mwachitsanzo, magazini a Galamukani! a mwezi wa December 2012 anamasuliridwa m’zinenero 84 ndipo magazini a Nsanja ya Olonda a mwezi wa December 2012 anamasuliridwa m’zinenero 195. Koma kuyambira mwezi wa January 2013 magazini a Galamukani! akumasuliridwa m’zinenero 98 ndipo magazini a Nsanja ya Olonda akumasuliridwa m’zinenero 204.

Magazini yophunzira ya Nsanja ya Olonda ipitiriza kukhala ndi masamba 32.

Nkhani za M’magazini Zachepa Koma za Pawebusaiti Zachuluka

Kuchepetsedwa kwa masamba a magazini a Galamukani! komanso Nsanja ya Olonda kukhudza webusaiti yathu ya www.jw.org m’njira ziwiri.

  1. Nkhani zina zimene zinkasindikizidwa m’magaziniwa zizipezeka pawebusaiti pokha. Mwachitsanzo, nkhani zakuti “Zoti Achinyamata Achite,” “Zimene Ndikuphunzira M’Baibulo,” “Mwambo wa Omaliza Sukulu ya Giliyadi,” “Zoti Banja Likambirane” komanso nkhani zakuti “Zimene Achinyamata Amadzifunsa,” zimene zinkapezeka mu Galamukani!, tsopano zizipezeka pawebusaiti pokha.

  2. Kwa zaka zambiri, magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! akhala akupezeka pawebusaiti yathu ya www.jw.org monga ma PDF. Tsopano magaziniwa azipezekanso pawebusatiyi monga ma HTML ndipo mungawapeze mosavuta komanso kuwawerenga pogwiritsa ntchito kompyuta kapena tizipangizo tina tamakono. Muzithanso kupeza mabuku ena amene akupezeka pawebusaitiyi m’zinenero zoposa 430.