Pitani ku nkhani yake

Kuthandiza Anthu Amene Ali ndi Vuto Losaona, ku Africa

Kuthandiza Anthu Amene Ali ndi Vuto Losaona, ku Africa

M’mayiko osauka, anthu amene ali ndi vuto losaona sakhala ndi mwayi umene anzawo a m’mayiko ena amakhala nawo. Anthu omwe ali ndi vutoli nthawi zina amasalidwa ndipo sathandizidwa moyenerera pa mavuto amene amakumana nawo okhudza mbali ya moyo imene anthu amene alibe vutoli sakumana ndi vuto lililonse. Mwachitsanzo, amavutika kupita kumsika, kukwera basi ndiponso kuwerengetsera ndalama. Iwo amavutikanso kuwerenga, chifukwa si onse amene amawerenga mabuku a zilembo za anthu amene ali ndi vuto losaona. Ngakhale atakhala kuti amawerenga mabuku a zilembozi, zimakhala zovuta kuti apeze mabukuwa m’zinenero zawo.

Kwa zaka zoposa 100, a Mboni za Yehova akhala akusindikiza mabuku othandiza kuphunzira Baibulo a m’zilembo za anthu omwe ali ndi vuto losaona. Pofuna kusindikiza mabuku a zilembozi m’Chichewa, chomwe chimalankhulidwa ku Malawi, a Mboni za Yehova kumeneko anaitanitsa makina osindikizira mabuku kuchokera kudziko la Netherlands.

Katswiri wina wokonza mabuku a m’zilembo za anthu omwe ali ndi vuto losaona, wa ku ofesi ya Mboni za Yehova ku Brazil dzina lake Leo, anapita ku Malawi kuti akathandize kagulu ka anthu 5, kugwiritsa ntchito makina osindikizira mabuku a m’zilembozi. Kuwonjezera pamenepa, anawaphunzitsanso mmene angagwiritsire ntchito pulogalamu ya pakompyuta yokonzera mabuku a zilembozi yomwe inapangidwa ndi a Mboni za Yehova. Kuti pulogalamuyi ichite zimenezi, zilembo zonse za pa afabeti ya Chichewa za anthu omwe alibe vuto losaona anaziika m’ndondomeko yofananiza ndi zilembo za pa afabeti ya Chichewa koma ya zilembo za anthu omwe ali ndi vuto losaona. Kenako pulogalamu ya pakompyutayi imasintha zilembo zoyambirirazo, zomwe zili m’mabuku, n’kupanga mabuku a zilembo za anthu omwe ali ndi vuto losaona kuti asamavutike kuwerenga. Tamvani zimene anthu ena ku Malawi anenapo zokhudza mabuku a m’zilembo za anthu omwe ali ndi vuto losaona.

Munyaradzi ndi mtsikana yemwe ali ndi vuto losaona ndipo amagwira ntchito kwa nthawi yochepa youlutsa mawu pawailesi. Komanso mwezi uliwonse mtsikanayu amaphunzitsa anthu ena Baibulo kwa maola 70. Iye anati: “M’mbuyomu ndinkalandira mabuku a Chingelezi othandiza pophunzira Baibulo, a zilembo za anthu omwe ali ndi vuto losaona. Koma panopa ndikusangalala chifukwa mabukuwa akupezeka m’Chichewa ndipo zimene ndikuwerenga zikundifika pamtima. Ndikuyamikira a Mboni anzanga chifukwa cha khama lawo potithandiza kuti tikhale ndi mabuku ophunzirira Baibulo, a zilembozi m’chinenero chathu. Izi zandithandiza kuona kuti sitinaiwalidwe ndiponso kuti ndife ofunika kwambiri.”

Francis ndi bambo wa Mboni za Yehova ndipo amakhala kumpoto m’dziko la Malawi. Chifukwa chakuti ali ndi vuto losaona, iye ankadalira anthu ena kuti azimuwerengera mabuku othandiza pophunzira Baibulo. Iye anasangalala kwambiri pa nthawi yoyamba imene analandira mabuku achichewa ophunzirira Baibulo, a zilembo za anthu omwe ali ndi vuto losaona. Francis anati: “Kodi ndikulota? Izitu n’zosangalatsa kwabasi!”

Loyce ndi mayi yemwe ali ndi vuto losaona ndipo amalalikira nthawi zonse. Anthu amene wawathandiza kusintha moyo wawo ndi okwana 52. Kodi mayiyu anakwanitsa bwanji zimenezi? Akamaphunzira ndi anthuwo, iye amagwiritsa ntchito mabuku azilembo za anthu amene ali ndi vuto losaona, ndipo anthu amene akuwaphunzitsawo amagwiritsa ntchito mabuku a zilembo za anthu amene alibe vutoli. Mabuku onsewa amapangidwa ndi a Mboni za Yehova.

Loyce akuphunzitsa munthu wina Baibulo

Leo yemwe anachokera ku Brazil ndipo tinamutchula kumayambiriro kwa nkhaniyi, anati: “Ndimasangalala kwambiri ndikathandizira anthu kuti alandire mabuku ophunzirira Baibulo m’zilembo za anthu amene ali ndi vuto losaona. Ndimanyadiranso ndikaona mmene anthu omwe ali ndi vutoli amasangalalira akalandira mabukuwa m’chinenero chawo. Anthu ambiri omwe ali ndi vutoli akuthokoza Yehova chifukwa cha mabukuwa ndiponso akusangalala chifukwa tsopano akumakonzekera okha misonkhano yachikhristu komanso ntchito yolalikira. Iwo sakufunikiranso munthu wina kuti aziwawerengera ndipo tsopano akumaphunziradi paokha. Panopa angathe kuthandiza mabanja mosavuta kuti azikonda kwambiri Mulungu. Chinanso n’chakuti mabukuwa akuwathandiza kuti akhale pa ubwenzi wabwino kwambiri ndi Yehova.”