Mayi ena achikulire dzina lawo a Odval, amakhala ku Mongolia ndipo sadziwa zaka zawo zenizeni koma amaganiza kuti anabadwa m’chaka cha 1921. Iwo sadziwa kuwerenga chifukwa ali mwana ankasamalira ziweto za makolo awo ndipo anangophunzira sukulu kwa chaka chimodzi basi. Koma posachedwapa kabuku ka zithunzi zokongola kawathandiza kudziwa Mulungu komanso kuphunzira zoti anthu amene amamvera Mulunguyo adzalandira moyo wosatha. Iwo amasangalala kwambiri chifukwa chophunzira zimenezi.

Kabuku kameneka, komwe kanapangidwa ndi a Mboni za Yehova, kanatuluka m’chaka cha 2011 ndipo kali m’mitundu iwiri. Timabuku tonse tili ndi zithunzi koma kena kali ndi mawu ambiri kuposa kanzake.

Posachedwapa, kabuku kamawu ambiri kotchedwa Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha kadzayamba kupezeka m’zinenero zokwana 583. Ndiponso kabuku kamawu ochepa kotchedwa Mverani Mulungu kazidzapezeka m’zinenero zokwana 483. Timabukuti tafalitsidwa m’zinenero zambiri poyerekeza ndi chikalata cha bungwe la United Nations chonena za ufulu wachibadwidwe chimene pofika mu October 2013, chinali chitamasuriridwa m’zinenero 413. Kuwonjezera pa kuchuluka kwa zinenerozi, chiwerengero cha timabuku ta Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha komanso Mverani Mulungu chafika pa 80 miliyoni.

Mayi winanso wachikulire wa ku Brazil anasangalala atalandira kabuku ka Mverani Mulungu ndipo anati: “N’zosangalatsa kudziwa kuti pali anthu ena amene amatiganizira. Sindinkalandira magazini anu chifukwa sinditha kuwerenga koma kabuku aka ndakakonda kwambiri.”

Nayenso Brigitte, yemwe ndi mayi wa ku France ndipo satha kuwerenga anati, “Tsiku lililonse ndimaona zithunzi za m’kabukuka.”

Wa Mboni wina ku South Africa, analemba kuti: “Kabukuka ndi kosavuta pokambirana nkhani za m’Baibulo ndi anthu olankhula Chitchainizi. Ndimakambirana ndi munthu aliyense, monga anthu ophunzira amene anapita kuyunivesite, komanso anthu amene satha kuwerenga. Kabuku kakuti Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha kamandithandiza kuphunzitsa mfundo za m’Baibulo mwa changu kwambiri.”

A Mboni ena ku Germany anayamba kuphunzira Baibulo ndi banja lina lophunzira kwambiri. Bambo wa m’banjali anachita chidwi ndi kabukuka ndipo anati: “Ndiye mwandipatsa mochedwatu. Kabukuka kakundithandiza kumvetsa mosavuta nkhani za m’Baibulo.”

Mayi wina wovutika kumva wa ku Australia anati: “Kwa zaka zambiri ndinkakhala ndi a sisitere. Ngakhale kuti nthawi zambiri ndinkakhala ndi atsogoleri a tchalitchi, palibe amene anandiphunzitsapo za Ufumu wa Mulungu. Koma zithunzi za m’kabukuka zandithandiza kumvetsa tanthauzo la lemba la Mateyu 6:10.”

Ofesi ya Mboni za Yehova ku Canada inalemba kuti: “Anthu omwe amakhala m’dera la anthu ochokera ku Sierra Leone anatiyamikira kwambiri ataona kabuku ka Mverani Mulungu m’chinenero cha Chikiliyo. Iwo anatiyamikira chifukwa choyesetsa kufalitsa uthenga wa m’Baibulo. Ndipo ena ananenanso kuti: ‘A Mboninu mumatikonda kwambiri kusiyana ndi anthu azipembedzo zina.’ ”