Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Webusaiti ya jw.org Tsopano Ili M’zinenero Zoposa 300!

Webusaiti ya jw.org Tsopano Ili M’zinenero Zoposa 300!

Mukadina pagawo la zinenero patsamba lino la pa jw.org, muona zinenero zochuluka zedi, zoposa 300. N’zokayikitsa ngati mungapeze mawebusaiti ena m’zinenero zochuluka chonchi.

Kodi mawebusaiti ena odziwika bwino akupezeka m’zinenero zingati? Taganizirani zotsatirazi: Pofika mu July 2013, webusaiti ya bungwe la United Nations inkapezeka m’zinenero 6 basi. Nayonso webusaiti ya Europa, yomwe ndi ya bungwe la European Union, imapezeka m’zinenero 24. Ndipo anthu angathe kulowa pa Google m’zinenero 71, pomwe pa Wikipedia anthu angalowepo m’zinenero 287.

Panapita nthawi yambiri kuti zitheke kumasulira webusaitiyi m’zinenero zoposa 300. A Mboni za Yehova padziko lonse ndi amene akugwira ntchito yaikuluyi, ndipo zimenezi zikuchititsa kuti Yehova azilemekezedwa. A Mboniwa amagwira ntchito m’timagulu pomasulira m’zinenero zosiyanasiyana kuchokera ku Chingelezi.

Webusaiti ya jw.org ili ndi masamba a nkhani ambirimbiri omwe akumasuliridwa m’zinenero zoposa 300. Zimenezi zimachititsa kuti chiwerengero cha masamba onse amene akupezeka pawebusaitiyi chikhale chokwera kwambiri, kuposa 200,000.

Kuwonjezera pa kupezeka m’zinenero zambiri, webusaiti ya jw.org ndi yotchukanso kwambiri. Zimenezi zikuonekera bwino tikaganizira lipoti la kampani ina yofufuza za kuchuluka kwa amene amalowa pa mawebusaiti osiyanasiyana, yotchedwa Alexa. Pagawo lake lakuti “Zipembedzo Ndiponso Kulambira” pali mawebusaiti pafupifupi 87,000, kuphatikizapo a zipembedzo zikuluzikulu padzikoli komanso a mabungwe osiyanasiyana a zipembedzo ofalitsa uthenga. Palipotilo, lomwe linatuluka mu July 2013, webusaiti ya jw.org inali panambala 2. Webusaiti yoyamba palipotilo inali webusaiti yamalonda, yomwe anthu amatha kufufuzapo Mabaibulo a m’zinenero zosiyanasiyana.

Pofika mu October 2013, anthu omwe amalowa pawebusaiti ya jw.org tsiku lililonse anali oposa 890,000. Tipitirizabe kuthandiza anthu kulikonse padziko lapansili kuti azitha kupeza uthenga wa m’Baibulo kwa ulele.

Onaninso

Kodi Ntchito Yolemba Ndiponso Kumasulira Mabuku Athu Imayenda Bwanji?

Timasindikiza mabuku m’zinenero zoposa 700. N’chifukwa chiyani timamasulira mabuku athu m’zinenero zambiri?