Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

Nsanja ya Olonda ya M’Chigirinilandi Inayamikiridwa pa TV

Nsanja ya Olonda ya M’Chigirinilandi Inayamikiridwa pa TV

Pofika mwezi wa January 2013, magazini ya Nsanja ya Olonda inali itafalitsidwa m’Chigirinilandi kwa zaka 40. Chigirinilandi n’chinenero cha ku Greenland ndipo chimalankhulidwa ndi anthu 57,000 okha basi.

Ku Greenland kuti anthu a Mboni za Yehova pafupifupi 150 basi koma mwezi uliwonse, magazini a Nsanja ya Olonda okwana 2,300 amafalitsidwa m’Chigirinilandi. Izi zikutanthauza kuti anthu ambiri amene amawerenga magaziniyi si a Mboni.

Munthu wina amene amayang’anira ofesi ya omasulira mabuku yomwe ili m’tauni ya Nuuk atafunsidwa ndi mtolankhani pa TV, ananena kuti: “Anthu ambiri ku Greenland kuno amawerenga Baibulo kwambiri ndipo n’chifukwa chake amakonda kuwerenga magazini ya Nsanja ya Olonda m’chinenero chawo.”

Mtolankhaniyo anafunsa munthu wina wa ku Greenland komweko amene amagwira ntchito yomasulira magaziniwa m’chinenerochi kuti anene chinthu chimene chimamusangalatsa kwambiri m’magaziniwo. Poyankha munthuyo ananena kuti: “Kuwerenga magazini amenewa kwandithandiza kwambiri pa moyo wanga. Mwachitsanzo ndaphunzira zimene ndingachite kuti ndikhale ndi moyo wabwino komanso wathanzi. Poyamba ndinkasuta fodya kwambiri ngakhale kuti ndinkadziwa zoti fodya amawononga moyo. Baibulo limanena kuti ngati tikufuna kukhala ndi moyo wathanzi, tikufunika kusamalira thupi lathu.

Pa pulogalamu ya pa TV imeneyo anaulutsanso kuti anthu a Mboni za Yehova akhala akugwira ntchito yawo ku Greenland kuyambira cha m’ma 1955 ndipo afalitsa mabuku ndi timabuku tambiri m’Chigirinilandi. Anthu ongodzipereka ochokera ku Denmark komanso Greenland komweko ndi amene amagwira ntchito yomasulirayi. Iwo amaonetsetsa kuti zimene akumasulira m’mabukumo zikumveka bwino ngati mmene anthu a ku Greenland amalankhulira chinenerochi.

Munthu wina amene wakhala wa Mboni za Yehova kwa nthawi yaitali ananena kuti: “Ndakhala ndikugwira ntchito yolalikira m’dziko lino kwa zaka 25 ndipo ndaona kuti anthu amasangalala kwambiri tikawapatsa mabuku a m’chinenero chawo. Pali midzi ina yakutali imene anthu angafikeko mwa apo ndi apo pachaka ndipo amapitako pa boti basi. Kumidzi imeneyi kuli anthu amene amakonda kuwerenga magazini athu choncho nthawi imene sitipitako, timangowatumizira makalata ndi mabuku.”

Kuyambira January 2013, magazini a Nsanja ya Olonda ophunzira ndi ogawira anayamba kufalitsidwa m’Chigirinilandi. Mukhoza kuwerenga kapena kukopera magaziniwa pawebusaiti ya jw.org. Pitani pamene alemba kuti “Mabuku” ndipo pagawo la chinenero sankhani Chigirinilandi.