Pitani ku nkhani yake

Chibaibulo Chachikulu Kwambiri

Chibaibulo Chachikulu Kwambiri

Mukafuna kupempha a Mboni za Yehova kuti akutumizireni Baibulo la zilembo za akhungu, muzionetsetsa kaye kuti muli ndi malo okwanira oti n’kulisungapo. Baibulo la Dziko Latsopano lathunthu la zilembo za akhungu, likupezeka m’Chingelezi, Chisipanishi ndiponso Chitaliyana. Mabaibulo a zilembo za akhungu m’zinenerozi anasindikizidwa m’mavoliyumu 18 mpaka 28 ndipo kuti muwasunge pashelefu, pamafunika malo osachepera mamita awiri.

Koma Mabaibulo a zilembo za akhungu amene ali pazipangizo zina zamakono m’malo molembedwa papepala, safuna malo ambiri. Mwachitsanzo, Mabaibulo ena angakhale pamakompyuta apadera a anthu akhungu omwe anthuwo amatha kulembapo kapena kuwerenga nkhani zimene zasungidwa pakompyutayo. Makompyutawa amathandiza kwambiri anthu akhungu chifukwa amathanso kusintha mawu olembedwa amene ali mukompyutayo n’kukhala omvetsera.

Komanso, a Mboni akonza pulogalamu inayake yapakompyuta imene imatha kusintha zilembo za zinenero zosiyanasiyana n’kukhala zilembo za akhungu. Pulogalamuyi imathanso kulemba zilembo za akhungu m’njira yoti anthu akhungu asavutike kuziwerenga. Pulogalamu imeneyi ithandizanso kuti mabuku a zinenero zosiyanasiyana, kuphatikizapo Baibulo, azituluka pafupifupi m’chinenero chilichonse chimene chili ndi zilembo za akhungu. Zinenero zimenezi zikuphatikizapo zinenero zimene zili ndi zilembo zovuta, monga Chitchainizi.

Kwa zaka zoposa 100, a Mboni za Yehova akhala akufalitsa mabuku ofotokoza nkhani za m’Baibulo m’zilembo za akhungu, ndipo panopa mabukuwa akupezeka m’zinenero 19. Ngakhale kuti anthu akhungu amene amachita chidwi ndi uthenga wa m’Baibulo angathe kulandira mabukuwa popanda kupereka ndalama iliyonse, ambiri amapereka ndalama mwakufuna kwawo zothandizira ntchitoyi.

M’mbuyomu pamsonkhano wa Mboni za Yehova pakatulutsidwa buku latsopano, anthu ankauzidwa kuti bukulo lidzayamba kupezeka m’zilembo za akhungu m’tsogolo muno. Koma chaka chathachi, ofesi ya Mboni za Yehova ya ku United States inachita kafukufuku m’mipingo kuti idziwe malo a misonkhano ikuluikulu amene anthu akhungu anakonza zoti akapezekepo. Ofesiyo inafunanso kudziwa ngati anthuwo angafune mabuku olembedwa pamapepala kapena pazipangizo zamakono.

Mabuku a m’zilembo za akhungu anatumizidwa kumisonkhano ikuluikulu imene kunali anthu akhungu. Zimenezi zinathandiza kuti anthu akhungu alandire mabuku amene anatulutsidwa pamisonkhanoyo. Patatha mlungu umodzi, mabuku azilembo za akhungu a pa zipangizo zamakono, anatumizidwa kwa munthu aliyense wakhungu amene anawaitanitsa.

Munthu wina wa Mboni yemwe ndi wakhungu anati: “Unali mwayi waukulu kulandira mabuku atsopano pa nthawi yofanana ndi imene anthu onse ankalandira mabuku awo. Lemba la Salimo 37:4 limati Yehova adzatipatsa zokhumba za mtima wathu. Iye wachitadi zimenezi pamsonkhano uno!” Munthu winanso analankhula akulira chifukwa chosangalala, kuti: “Kodi inenso amandiwerengera eti? Zikomo kwambiri Yehova potisamalira mwachikondi chonchi.