ANTHU ovutika kumva anakweza manja m’mwamba poyamikira atamva chilengezo chosangalatsa chakuti: “Musangalala kudziwa kuti ntchito yomasulira ena mwa mabuku a m’Baibulo a Malemba Achiheberi [Chipangano Chakale] ili mkati. Panopa, vidiyo ya buku la Genesis yatha kale!

Chilengezo chimenechi chinaperekedwa mkati mwa nkhani yomaliza ya pamsonkhano wina wa Mboni za Yehova wa chaposachedwapa. Chilengezochi chinaperekedwa m’Chinenero Chamanja cha ku America (ASL).

Mu 2005, a Mboni za Yehova anayamba ntchito yomasulira Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika m’Chinenero Chamanja cha ku America, ndipo anayambira ndi buku la Mateyu. Pofika mu 2010, mabuku onse 27 amene anthu ena amangoti a Chipangano Chatsopano anali atatha.

Kuwonjezera pamenepa, a Mboni za Yehova amasulira zigawo zina za Baibulo m’zinenero 5 zinanso zamanja.

N’chifukwa chiyani akugwira ntchito yonseyi? A Mboni za Yehova amazindikira kuti anthu ambiri ovutika kumva sangathe kuwerenga kapena kumva uthenga umene ungakhale m’Baibulo lochita kusindikiza. Choncho, Baibulo la m’chinenero chamanja lomasuliridwa molondola komanso momveka bwino, limathandiza anthu ambiri ovutika kumva kuti amvetse uthenga wa m’Baibulo komanso kuti alimbitse ubwenzi wawo ndi Mulungu. Kodi anthu alilandira bwanji Baibulo limeneli?

Mnyamata wina wovutika kumva anati: “Buku la Mateyu litatulutsidwa zaka zingapo m’mbuyomo, ndinaona kuti umenewu ndi umboni wakuti Yehova Mulungu amandikonda monga munthu pandekha. Ndipo buku la Genesis langowonjezera chisangalalo changa. N’zoonekeratu kuti Yehova akundithandiza kuti ndimudziwe bwino.

Mayi wina yemwenso ndi wovutika kumva anayamikira kwambiri ponena mawu otsatirawa: “Apa zikuchita kuonekeratu kuti Yehova akufuna kuti ndiziwerenga Mawu ake monga nkhani komanso vesi ndi vesi n’cholinga choti ndimudziwe bwino. Zimenezi zandikhudza mtima kwambiri ndipo zandithandiza kuti ndizipemphera kuchokera pansi pa mtima. Masiku ano ndikukonda kuwerenga Baibulo kwambiri.