Pitani ku nkhani yake

Mafamu a Watchtower Akhala Akuthandiza Kwambiri kwa Zaka 50

Mafamu a Watchtower Akhala Akuthandiza Kwambiri kwa Zaka 50

Mukayenda mtunda wa makilomita pafupifupi 145 kuchokera mumzinda wa New York City n’kumalowera chakumpoto, mumafika pamafamu amene ali pafupi ndi tauni ya Wallkill, m’chigawo chomwecho cha New York. Mafamu amenewa akhala akuthandiza kwambiri pa ntchito imene a Mboni za Yehova amagwira, yophunzitsa anthu Baibulo padziko lonse. Famu yoyambirira pamafamuwa, omwe masiku ano amatchedwa kuti Mafamu a Watchtower, inagulidwa zaka 50 zapitazo, pa January 2, 1963.

Bambo David Walker, omwe ndi a Mboni za Yehova ndipo akhala akutumikira ku Wallkill kuyambira pamene famu yoyambirirayi inagulidwa, anati: “Chiwerengero cha anthu ogwira ntchito kulikulu la Mboni za Yehova lomwe lili ku Brooklyn, m’chigawo cha New York, chinkachuluka kwambiri ndipo pankafunika kupeza njira yosawononga ndalama zambiri yopezera chakudya chodyetsera anthu amenewa. Famu ina imene a Mboni za Yehova ankalimako zakudya zawo inali kutali kwambiri chakumpoto kwa New York moti anthu ankafunika kuyenda pagalimoto kwa maola 6 kapena 8 kuti akafike kufamuyi kuchokera ku Brooklyn. Koma kuti munthu afike ku Wallkill kuchokera ku Brooklyn amayenda maola awiri okha pagalimoto. Choncho tinaona kuti famu ya ku Wallkill ili pamalo abwino kwambiri.” Patapita nthawi, a Mboni za Yehova anayamba kulima ndiwo zamasamba ndi zipatso pafamuyi. Komanso anayamba kuweta nkhuku, nkhumba ndi ng’ombe pafamu yomweyi, ndipo izi zinathandiza kuti azipeza mosavuta nyama ndi mkaka. N’kupita kwa nthawi, anawonjezera mafamu enanso.

Zaka 10 zisanathe, zinthu zina zinawonjezeredwa kumafamu a ku Wallkill chifukwa choti anthu a Mboni za Yehova padziko lonse amachulukirachulukira. Kuwonjezera pa kulima mbewu zenizeni zomwe zingakololedwe, kunayambikanso ntchito ina yopanga mabuku othandiza pa ntchito yokolola imene Yesu anaitchula. (Mateyu 9:37; Luka 10:2; Yohane 4:35, 36) Taonani zina mwa ntchito zimene zakhala zikuchitika ku Wallkill.

Ntchito Yosindikiza Mabuku: M’zaka za m’ma 1950, mabuku ambiri ofotokoza nkhani za m’Baibulo amene amakonzedwa ndi a Mboni za Yehova ankasindikizidwa ku Brooklyn, ku New York. Koma chifukwa choti anthu amene ankafuna mabukuwa anachuluka, panafunika kukhala nyumba zina zosindikizira mabuku. Choncho m’chaka cha 1973, a Mboni za Yehova anamaliza kumanga nyumba zina zosindikizira mabuku ku Wallkill. Kuchokera nthawi imeneyi, nyumba zosindikizira mabukuzi zakhala zikukulitsidwa maulendo angapo, ndipo nthawi yomaliza imene nyumbazi zakulitsidwa ndi chaka cha 2004.

Luso la za Makompyuta: M’chaka cha 1979, kagulu ka anthu ena a Mboni za Yehova ku Wallkill kanayamba kukonza pulogalamu ya pa kompyuta yotchedwa Multilanguage Electronic Publishing System (MEPS). Pulogalamu imeneyi imathandiza kuti mabuku ofotokoza nkhani za m’Baibulo azimasuliridwa m’zinenero zoposa 600.

Maphunziro: M’chaka cha 1988, Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo inasamutsidwa ku Brooklyn kupita ku Wallkill ndipo makalasi anayamba pa October 17 chaka chomwecho. Mu April 1995, sukuluyi inasamutsidwira ku Likulu la Maphunziro la Watchtower lomwe lili ku Patterson, mumzinda wa New York.

Mofanana ndi mafamu ena, Mafamu a Watchtower akhala akusintha m’njira zosiyanasiyana pa zaka 50 zapitazi. Komabe ayesetsa kuti azitha kukolola chakudya chopatsa thanzi cha anthu a Mboni za Yehova amene akutumikira ku nyumba za Beteli zomwe zili ku New York, m’dziko la United States.

Pakali pano, a Mboni za Yehova akumanga maofesi atsopano, nyumba zogona ndi nyumba zina ku Wallkill. Iwo akukonzanso nyumba zimene zinamangidwa kale kumalowa. Ntchito yonseyi ithandiza kuti Mafamu a Watchtower apitirize kupereka zinthu zofunika zimene zingathandize anthu ochuluka a Mboni za Yehova kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova.

Bambo David Walker, amene tawatchula kale m’nkhaniyi ananena kuti: “Kwa zaka 50 zapitazi, ndakhala wosangalala kwambiri kuona mmene nyumba ndi mafamu a ku Wallkill akulira komanso mmene athandizira pa ntchito yathu ya padziko lonse yophunzitsa anthu uthenga wa m’Baibulo.”