Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

Ulendo Wosaiwalika

Ulendo Wosaiwalika

Chaka chilichonse anthu masauzande ambirimbiri amabwera kudzaona malo kunyumba zomwe ndi maofesi a Mboni za Yehova a ku United States komanso maofesi omwe ndi likulu la Mboni za Yehova padziko lonse. Nyumba zimenezi zili m’chigawo cha New York. Maofesiwa amatchedwa Beteli, dzina la Chiheberi lomwe limatanthauza “Nyumba ya Mulungu.” Ena mwa anthuwo amachokera kutali kwambiri ndipo amabwera kudzaona mmene mabuku athu amasindikizidwira, mmene ntchito yathu imayendera komanso kudzaona achibale awo amene amagwira ntchito kumaofesiwa. Munthu wina yemwe anabwera kudzaona malowa posachedwapa, anakonzekera ulendowu kwa nthawi yaitali.

Bambo Marcellus omwe ndi a Mboni za Yehova amakhala ku Anchorage, m’dera la Alaska, m’dziko la United States. Bambowa amalankhula mawu ochepa chabe chifukwa cha matenda opha ziwalo amene anadwala zaka zingapo zapitazo. * Iwo amayenda pa njinga ya anthu olumala ndipo amafunika kumawathandiza pa ntchito za tsiku ndi tsiku. Ngakhale izi zili chonchi, bambowa ankafunitsitsa kukaona ku Beteli. Chaposachedwapa, zimene bambowa ankafuna zinatheka.

Bambo Corey, omwe ndi mnzawo wa Marcellus, ndipo ankawathandiza pokonzekera ulendowu, anati: “Anali kundikumbutsa mobwerezabwereza za ulendowu. Ankandiimbira foni pafupipafupi kuti andifunse zina n’zina zokhudzana ndi ulendowu. Popeza amavutika kulankhula, nthawi zambiri amangoyankha kuti ‘Inde’ kapena ‘Ayi’ basi. Ndiyeno akandiimbira foni ndinkafunika kuwafunsa mafunso osiyanasiyana.” Ankacheza chonchi:

“Kodi mukufuna kuti ndibwere?”

“Ayi.”

“Kodi ndiitane adokotala?”

“Ayi.”

“Kapena mukufuna kudziwa zokhudza ulendo uja?”

“Inde.”

“Ndiyeno ndinkafunika kufotokoza zimene ndachita pokonzekera ulendowo. Ndinasangalala kwambiri kuona kuti zimene ankafuna zinathekadi.”

Bambo Marcellus analimbana ndi mavuto ambiri kuti ulendowu utheke. Popeza amapeza ndalama movutikira, iwo ankafunika kusunga ndalama kwa zaka ziwiri kuti adzakwanitse kulipira ulendo wamakilomita 5,400, kuchokera kwawo ku Alaska kukafika ku New York. Chifukwa cha kulumala kwawo, iwo ankafunikanso kupeza munthu wodalirika kuti awaperekeze pa ulendowu. Komanso ankafunika kuti dokotala wawo awavomereze ngati angathe kupita, ndipo iwo analandira yankho lochokera kwa dokotalayu kutangotsala masiku ochepa kuti ulendowu uchitike.

A Marcellus atangofika ku New York anaona maofesi a ku Brooklyn, Patterson, ndi ku Wallkill. Iwo anaona makina aakulu osindikizira mabuku ndi Mabaibulo ndiponso anadziwa mmene ntchito yathu imayendera. Iwo anaonanso malo oonetsera zinthu zosiyanasiyana. Mbali ina ya malowo kuli mawu akuti “Dzina la Mulungu M’Baibulo,” ndipo mbali ina kuli mawu enanso akuti, “Anthu Odziwika ndi Dzina la Yehova.” Pa ulendowu, a Marcellus anadziwana ndi anthu ambiri. Zoonadi, umenewudi unali ulendo wosaiwalika!

Anthu ambiri amagoma akapita kukaona malo ku Beteli, ndipo akafunsidwa kuti afotokoze zimene aona, amachita kusowa chonena. Koma a Marcellus atafunsidwa ngati anasangalala ndi ulendo wawo wokaona Beteli, anangoyankha ndi mawu omwe aja akuti: “Inde. Inde. Inde!”

Inunso pamodzi ndi banja lanu mungalimbikitsidwe kwambiri ngati mupita kukaona Beteli monga mmene anachitira Bambo Marcellus. Maofesi athu akupezeka m’mayiko ambiri padziko lonse ndipo aliyense ndi wolandiridwa kudzaona malo. Tayesetsani kubwera kuti mudzaone Beteli.

^ ndime 3 Bambo Marcellus anamwalira pa May 19, 2014, pomwe tinkakonzekera kufalitsa nkhani ino.