Kuchokera mu 2013, pamene tinatsegulira malo athu oonetsera Mabaibulo osiyanasiyana, takhala tikulandira Mabaibulo akale ndiponso ofunika kwambiri. Tinapatsidwa Mabaibulo monga Complutensian Polyglot ndiponso Mabaibulo akalekale a King James Bible ndi Erasmus’ Greek “New Testament.”