Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

Kulondile ya pa Beteli Amachapa Chilichonse

Kulondile ya pa Beteli Amachapa Chilichonse

Pamaofesi a Mboni za Yehova m’dziko la United States pali achinyamata amene anadzipereka kuti azigwira ntchito yochapa zovala kulondile. Chaka chilichonse, iwo amachapa zovala zolemera matani 1,800, ndipo amagwira ntchitoyi kumalondile a kumaofesi omwe ali ku Brooklyn, Patterson ndi ku Wallkill m’dera la New York. Ntchito yochapayi ndi yaikulu komanso yochititsa chidwi kwambiri. Tikutero chifukwa kumalondile amenewa amachapa zinthu zosiyanasiyana.

Tsiku lililonse kuyambira Lolemba mpaka Lachisanu, anthu amene amakhala ku Beteli m’dziko la United States amatumiza zovala zoposa 11,000 kulondile kuti zichapidwe. Pazovala zimenezi pamakhala mashati oposa 2,300, mathalauza 650, matisheti, masokosi ndiponso zovala zamkati. Komanso tsiku lililonse amachapa zovala zina monga masuti, zokwana 900 kulondile yosagwiritsa ntchito madzi.

Kuwonjezera pa zovalazi, tsiku lililonse amachapanso zinthu zina zambirimbiri monga nsalu, matawelo, mabulangete, mayunifolomu a anthu operekera zakudya ndiponso tinsalu topukutira zinthu. Zinthu zonsezi zimachapidwa, kuumitsidwa ndiponso kukasiidwa kumalo ake oyenerera. Zinthu ngati tinsalu topukutira zimachapidwa zambirimbiri nthawi imodzi. Koma zinthu ngati mataye ndi mabulauzi ena zimachapidwa chilichonse pachokha.

Anthu amene amagwira ntchito kulondile amaonetsetsa chovala chilichonse kuti aone ngati chang’ambika kapena chathothoka mabatani. Akapeza chovala chothothoka mabatani, amachiika m’makina amene amaikirira mabatani ndipo nthawi zina amaika mabataniwo pamanja. Akapeza chovala chong’ambika kapena chofunika kukonza penapake, akatswiri odziwa kusoka amachisoka.

Pofuna kuti zovala zisasokonezeke, munthu aliyense wa m’banja la Beteli ku United States amakhala ndi nambala yapadera. Anthu a kulondile amagwiritsa ntchito makina n’kumata nambalayo pachovala chilichonse cha munthuyo. Zimenezi zimathandiza kuti zovala zikachapidwa komanso kusitidwa, ziziperekedwa kwa mwini wake weniweni.

Munthu amene wangoyamba kumene kugwira ntchito kulondile amaphunzitsidwa ndi anthu aluso amene agwira ntchitoyi kwa nthawi yaitali. Munthu watsopanoyo angathe kuphunzitsidwa zinthu zosiyanasiyana zokwanira 20 zokhudzana ndi kuchapa zovala. Mwachitsanzo, amaphunzitsidwa ntchito yooneka ngati yophweka, yochotsa timadontho timene tingathimbiriritse chovala. Munthuyo amaphunzitsidwanso kuti azidziwa bwino nsalu zosiyanasiyana zimene anasokera chilichonse ndiponso njira yoyenerera imene angachapire zovala zoterozo.

M’bale wina dzina lake Tajh, yemwe wagwira ntchito kulondile kwa chaka chimodzi ndi hafu, ananena za anthu amene amagwira nawo ntchito kuti: “Ndikugwira ntchito ndi anthu abwino kwambiri. Kugwira ntchito ndi anthu a zikhalidwe zosiyanasiyana n’chinthu zosangalatsa kwabasi.” Mlongo wina dzina lake Shelly, amenenso amagwira ntchito kulondile, anati: “Ndimwayi wapadera kugwira nawo ntchito yothandiza kuti anthu a m’banja la Beteli azioneka bwino.”