Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

Tikukuitanani Kuti Mudzaone Maofesi Athu ku United States

Tikukuitanani Kuti Mudzaone Maofesi Athu ku United States

“Sitidzaiwala zomwe taona kuno ku Beteli mpaka kalekale.” Amenewa ndi mawu omwe banja lina lochokera kuchilumba cha Vanuatu linanena, litamaliza kuona maofesi athu ku United States. N’zomwenso anthu oposa 70 000 omwe amabwera chaka chilichonse kudzaona maofesiwa, amanena.

Kodi inuyo munabwera kudzaona maofesi athu a ku United States? Ngati simunawaone tikukuitanani ndipo tidzakulandirani mosangalala.

Kodi ku maofesiwa mudzaona zotani?

Zimene mudzaone ku Likulu la Padziko Lonse ku Brooklyn, New York. Mukadzafika kumaofesiwa mudzakhala ndi mwayi woona zimene anthu ogwira ntchito kumalowa amachita pofuna kuthandizira ntchito yolalikira yomwe ikuchitika padziko lonse. Mudzaonanso malo awiri osonyeza zinthu zosiyanasiyana zokhudza mbiri ya Mboni za Yehova. Malo oyamba anapatsidwa mutu wakuti “Anthu Odziwika ndi Dzina la Yehova,” ndipo amasonyeza mbiri ya anthu a Yehova kuyambira nthawi ya atumwi mpaka masiku ano. Malo ena anawapatsa mutu wakuti “Dzina la Mulungu M’Baibulo,” ndipo akusonyeza Mabaibulo ambiri amene ali ndi dzina la Mulungu.

Zimene mudzaone ku Likulu la Maphunziro ku Patterson, mumzinda wa New York. Mukadzafika kumalowa, mudzaona sukulu zosiyanasiyana monga Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo komanso Sukulu ya Abale a M’komiti ya Nthambi ndi Akazi Awo. Mudzaonanso zinthu ndi mavidiyo osonyeza ntchito imene imachitika m’maofesi a madipatimenti osiyanasiyana monga dipatimenti yojambula zithunzi, dipatimenti yojambula mavidiyo ndi mawu, dipatimenti yoona zamalamulo ndi dipatimenti ya utumiki.

Zimene mudzaone ku Malo Osindikizira Komanso Kutumizira Mabuku omwe ali ku Wallkill, mumzinda wa New York. Mudzaona mmene Mabaibulo komanso mabuku othandiza pophunzira Baibulo amasindikizidwira, kumatidwa komanso kutumizidwa m’mipingo ya ku United States, Caribbean komanso m’madera ena padziko lapansi.

Kodi kuona malo kumatenga nthawi yaitali bwanji?

Ku Brooklyn pafupifupi ola limodzi, ku Patterson pafupifupi maola awiri ndipo ku Wallkill pafupifupi ola limodzi ndi hafu.

Kodi ndi ndani amaonetsa malowa?

Anthu amene amagwira ntchito m’madipatimenti osiyanasiyana ku Beteli. Amaona kuti kuonetsa anthu malowa ndi mbali ya ntchito yawo yophunzitsa anthu padziko lonse. Mu May 2014, anthu amene ankagwira ntchito m’malo onse atatuwa anali oposa 5,000 ndipo 3,600 mwa anthuwa anaphunzitsidwa kuti azionetsa anthu malowa. Anthuwa amagwiritsa ntchito zinenero pafupifupi 40 poonetsa malowa.

Kodi munthu amapereka ndalama zingati kuti aone malowa?

Munthu amaona malowa kwaulere.

Kodi ndi a Mboni okha amene amaona malowa?

Ayi ndithu. Anthu ambiri amene amadzaona malowa si a Mboni. Anthu omwe ndi a Mboni komanso omwe si a Mboni akadzaona malowa, amadziwa zambiri za mmene ntchito ya a Mboni za Yehova ya padziko lonse imayendera.

Mayi wina wachisilamu nthawi ina anakaona malo ku Patterson. Atamaliza kuona malowa ananena kuti: “Ndikanakonda ndikanakhala ngati inuyo. Zikomo kwambiri pondisonyeza ulemu waukulu chonchi.”

Kodi ananso amaloledwa kuona malowa?

Kwambiri. Ndipo zimene ana angaone zikhoza kukhudza moyo wawo wonse. Munthu wina wa ku United States amene anakaona nawo malowa dzina lake John, analemba kuti: “Ana amene tinakaona nawo malowa sasiya kunena zinthu zosangalatsa zimene anaona. Tisanakaone malowa, sankadziwa kuti moyo wa pabeteli ndi wotani. Koma panopa ali ndi cholinga chofuna kukatumikira pabeteli.”

Kodi n’zotheka kuona maofesi a Mboni za Yehova omwe ali m’mayiko ena?

Inde n’zotheka. M’mayiko onse kumene kuli maofesi athu, anthu amaloledwa kuona malo. Ngati mukufuna kudziwa kumene kuli maofesi athu m’dziko lanu, tsegulani tsamba lakuti Maofesi ndi Kuona Malo. Tidzakulandirani ndi manja awiri mukadzabwera kudzaona maofesi athu.