Pitani ku nkhani yake

Famu Yomwe Ikudyetsa Anthu Mamiliyoni

Famu Yomwe Ikudyetsa Anthu Mamiliyoni

Zaka 40 zapitazo, pa February 2, 1973, a Mboni za Yehova anaika makina atsopano osindikizira mabuku ku Wallkill, m’dera la New York m’dziko la United States, n’cholinga choti azisindikiza magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!

Zaka 10 m’mbuyomo izi zisanachitike, a Mboni za Yehova anagula malowa n’cholinga choti akhale famu yoti azilimapo chakudya cha anthu amene amagwira ntchito kulikulu lawo lomwe lili ku Brooklyn, mumzinda wa New York. Koma mu 1973, anakonza zoti malowa ayambe kugwiritsidwanso ntchito pokonza chakudya cha mtundu wina, chomwe ndi chauzimu.​—Mateyu 24:​45-47.

Famu ya Watchtower, ku Wallkill, m’dera la New York, chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 1970.

Bambo Philip Wilcox, omwe pa nthawiyo ankayang’anira ntchito yosindikizayo anafotokoza zimene zinachitika patsiku limene makinawo ayamba kugwira ntchito ku Wallkill. Iwo anati: “Zinatitengera pafupifupi mwezi wathunthu kuti tiike makinawa, omwe ndi amphamvu komanso apamwamba zedi. Koma kenako zonse zinali m’malo ndipo tinayamba kuyeserera kuwagwiritsa ntchito. Pasanapite nthawi, tinasindikiza magazini masauzande angapo. Tinatumiza magaziniwo ku ofesi yathu yosindikizira mabuku yomwe inali ku Brooklyn, ndipo kumeneko anawatumiza m’mipingo. Ngakhale kuti tinasindikiza magaziniwa poyesa makinawo, tinatumizabe magaziniwo kumipingo.”

A Mboni za Yehova anamanga malo osindikizira mabuku atsopanowa kuti azisindikiza magazini ena kuwonjezera pa omwe ankasindikizidwa ku Brooklyn. Chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 1970, anthu ambiri ankafuna mabuku ofotokoza nkhani za m’Baibulo choncho panafunika kuti mabuku ambiri azisindikizidwa. Kuti izi zitheke, anthu ogwira ntchito kunyumba yosindikizira mabuku ya ku Brooklyn anakonza zoti anthu ena azigwiranso ntchito usiku kuti azisindikiza mabuku ambiri.

Pamwamba: Mu January 1973. Ku Wallkill, akuika makina oyambirira otchedwa M.A.N. M’munsi: Akuika mapepala m’makina osindikizira otchedwa M.A.N.

Nyumba yoyamba yosindikizira mabuku itatha kumangidwa ku Wallkill, mkati mwake munali holo ndi maofesi a dipatimenti yotumiza mabuku kumipingo, Nyumba ya Ufumu, ndiponso makina anayi osindikiza mabuku. Ngakhale kuti ntchito yosindikizayo inali isanafike pachimake, panayambikanso ntchito yomanga nyumba ina yaikulu kwambiri, yomwe anailumikiza kunyumba yoyamba ija. Popeza anthu ochuluka zedi ankafuna mabuku athu ofotokoza nkhani za m’Baibulo, m’nyumba yachiwiriyi anaikamo makina ena 6 osindikizira mabuku ngakhale kuti pa nthawiyi n’kuti nyumbayo isanathe kwenikweni.

Kuchokera pa nthawi imeneyo, luso lamakono lakhala likupita patsogolo komanso anthu omwe amafuna mabuku athu ofotokoza nkhani za m’Baibulo akhala akuwonjezereka. Kuti tigwirizane ndi kusintha kwa zinthu kumeneku, takhala tikukulitsa nyumba zosindikizira mabuku zomwe zili ku Wallkill komanso takhala tikusintha makina osindikizira. Mwachitsanzo, m’zaka za m’ma 1980, tinachotsa makina akale omwe tinkasindikizira mabuku n’kuika makina atsopano amphamvu kwambiri.

Mu 2004, tinasiya kusindikiza mabuku ku Brooklyn ndipo kwa nthawi yoyamba, mabuku anayamba kusindikizidwa ku Wallkill kuwonjezera pa magazini. Mu 2010, ntchito yosindikiza magazini inasamutsidwira chakumpoto, ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova m’dziko la Canada. Makina atsopano amene ali ku ofesi ya nthambi imeneyi angathe kusindikiza magazini 200,000 pa ola limodzi.

Pamwamba: Mu 2005. Ku Wallkill, akulongedza mapepala opangira buku limodzi kuti awamate. M’munsi: Mu 2013. Famu ya Watchtower, ku Wallkill m’dera la New York.

Masiku ano, kumalo osindikizira mabuku amene ali ku Wallkill kuli makina amakono komanso apamwamba kwambiri ndipo anthu okwana 281 amagwira ntchito pamalowa mongodzipereka. Chaka chatha anasindikiza mabuku ndi Mabaibulo oposa 17 miliyoni. Kuwonjezera pamalo osindikizira mabuku amene ali ku Canada ndi ku Wallkill m’chigawo cha North America, a Mboni za Yehova alinso ndi malo ena 13 osindikizira mabuku, amene amathandiza kudyetsa anthu mamiliyoni ambirimbiri chakudya chauzimu. Malo amenewa ali m’madera osiyanasiyana monga ku Africa, ku Asia, ku Australia, ku Ulaya ndiponso ku South America.​—Mateyu 5:3.