Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

Kodi Ndani Anayambitsa Chipembedzo Chanuchi?

Kodi Ndani Anayambitsa Chipembedzo Chanuchi?

Gulu la masiku ano la Mboni za Yehova linayamba chakumapeto kwa zaka za m’ma 1800. Pa nthawiyo, kagulu ka ophunzira Baibulo amene ankakhala pafupi ndi mzinda wa Pittsburgh, ku Pennsylvania, m’dziko la United States, kanayamba kuphunzira ndiponso kukambirana mfundo za m’Baibulo mwakhama kwambiri. Iwo ankayerekezera zimene matchalitchi ankaphunzitsa ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. Kenako zimene ankaphunzirazo anayamba kuzifalitsa m’mabuku, manyuzipepala ndiponso m’magazini imene masiku ano imadziwika ndi dzina lakuti Nsanja ya Olonda—Yolengeza Ufumu wa Yehova.

Pagulu la anthu amene ankaphunzira Baibulo mwakhamawo panali munthu wina dzina lake Charles Taze Russell. Ngakhale kuti Russell ankatsogolera pa ntchito yophunzitsa anthu Baibulo yomwe inkachitika pa nthawiyo komanso anali mkonzi woyambirira wa Nsanja ya Olonda, iye si amene anayambitsa chipembedzo chatsopanocho. Cholinga cha Russell komanso anzakewo, omwe onse pa nthawiyo ankadziwika ndi dzina lakuti Ophunzira Baibulo, chinali kulimbikitsa mfundo zimene Yesu Khristu ankaphunzitsa komanso kutsanzira zimene mpingo wa Akhristu oyambirira unkachita. Popeza Yesu ndi amene anayambitsa Chikhristu, timaona kuti Yesuyo ndi amene anayambitsa gulu lathu.—Akolose 1:18-20.