Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

Kodi Ndinu Gulu Lampatuko la ku America?

Kodi Ndinu Gulu Lampatuko la ku America?

Likulu lathu limene limayang’anira ntchito ya padziko lonse lili ku United States of America. Koma si ndife gulu lampatuko la ku America pa zifukwa zotsatirazi:

  • Anthu ena amati gulu lampatuko limachita kuchoka m’chipembedzo china chachikulu kapena chodziwika bwino. Koma a Mboni za Yehova sanachite kuchoka m’chipembedzo china. M’malomwake, timaona kuti tinakhazikitsanso Chikhristu chimene chinalipo m’nthawi ya atumwi.

  • A Mboni za Yehova akugwira ntchito yawo yolalikira mwakhama m’mayiko oposa 230. M’dziko lililonse limene tikukhala, timaonetsetsa kuti choyamba, tikumvera ndiponso kugonjera Yehova Mulungu ndi Yesu Khristu, osati boma la ku America kapena boma lina lililonse la anthu.—Yohane 15:19; 17:15, 16.

  • Mfundo zonse zimene timaphunzitsa zimachokera m’Baibulo, osati kwa mtsogoleri wina wachipembedzo wa ku United States.—1 Atesalonika 2:13.

  • Ife timatsatira Yesu Khristu, osati mtsogoleri winawake.Mateyu 23:8-10.