Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Kodi Muli ndi Amishonale?

Kodi Muli ndi Amishonale?

Inde. Kulikonse kumene tili, anthu tonse a Mboni za Yehova timayesetsa kukhala ndi mtima waumishonale, kutanthauza kuti nthawi zonse timayesetsa kuuza ena zimene timakhulupirira.—Mateyu 28:19, 20.

Kuwonjezera pamenepa, anthu ena a Mboni nthawi zambiri amapita kapena kusamukira m’madera ena a m’dziko lawo lomwelo, kumene anthu ambiri sanamvepo uthenga wabwino wa m’Baibulo. Koma a Mboni ena amasamukira m’mayiko ena n’cholinga choti azikalalikira uthenga wabwino. Iwo amasangalala kuchita zimenezi chifukwa amathandiza pokwaniritsa ulosi umene Yesu ananena kuti: “Mudzakhala mboni zanga . . . mpaka kumalekezero a dziko lapansi.”—Machitidwe 1:8.

Mu 1943, tinatsegula sukulu yophunzitsa anthu ntchito ya umishonale. Kuyambira m’chaka chimenecho, anthu a Mboni oposa 8,000 aphunzitsidwa kusukulu imeneyi, yomwe imadziwika ndi dzina lakuti Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo.

 

Onaninso

Sukulu ya Giliyadi Yakwanitsa Zaka 70

Pa February 1, 1943, kalasi yoyamba ya sukulu yapadera kwambiri inayamba m’dera la kumpoto ku New York. Sukuluyi yathandiza anthu masauzande ambiri kuti azigwira ntchito yolalikira komanso kuphunzitsa ena za Mulungu.

Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo—Mwambo wa Omaliza Maphunziro a Kalasi Nambala 134

Ophunzira a m’kalasi nambala 134 a Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo anamaliza maphunziro awo pa March 9, 2013. Pamwambowu panakambidwa mfundo zosonyeza mmene sukuluyi ikuthandizira pa ntchito yolalikira kuchokera pamene anaitsegulira zaka 70 zapitazo.