Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

Kodi Mumakhulupirira Kuti Ndinu Nokha Amene Mudzapulumuke?

Kodi Mumakhulupirira Kuti Ndinu Nokha Amene Mudzapulumuke?

Ayi. Tikutero chifukwa anthu mamiliyoni ambiri amene anakhalapo zaka zambirimbiri m’mbuyomu amene sanali a Mboni za Yehova ali ndi mwayi wodzapeza moyo wosatha. Baibulo limafotokoza kuti m’dziko latsopano limene Mulungu walonjeza, “kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.” (Machitidwe 24:15) Komanso anthu ambiri amene ali ndi moyo panopa akhoza kuyamba kutumikira Mulungu, ndipo nawonso angadzapulumuke. Ndipotu si udindo wathu kuweruza kuti anthu awa adzapulumuka kapena ayi. Udindo umenewu ndi wa Yesu.—Yohane 5:22, 27.