Ayi. Ife a Mboni za Yehova ndife Akhristu koma chipembedzo chathu si cha Chipulotesitanti. N’chifukwa chiyani tikutero?

Zipembedzo za Chipulotesitanti ndi zomwe “zimatsutsa chipembedzo cha Roma Katolika.” Ngakhale kuti ife a Mboni za Yehova sitigwirizana ndi zimene tchalitchi cha Katolika chimaphunzitsa, timaona kuti sitili m’gulu la zipembedzo za Chipulotesitanti pa zifukwa zotsatirazi:

  1. Zinthu zambiri zimene anthu a zipembedzo za Chipulotesitanti amakhulupirira sizigwirizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. Mwachitsanzo, Baibulo limaphunzitsa kuti “pali Mulungu mmodzi,” osati milungu itatu mwa Mulungu m’modzi. (1 Timoteyo 2:5; Yohane 14:28) Baibulo limanenanso momveka bwino kuti Mulungu amalanga anthu oipa, osati powawotcha kumoto, koma ndi “chiwonongeko chamuyaya.”Salimo 37:9; 2 Atesalonika 1:9.

  2. Sitiumiriza tchalitchi cha Katolika kapena tchalitchi chilichonse kuti chisinthe zimene chimakhulupirira. M’malomwake, timangolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu n’kumathandiza ena kuti azikhulupirira zimene uthenga wabwinowo umanena. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Ife cholinga chathu sikusintha zimene zipembedzo zina zimakhulupirira koma kuphunzitsa munthu aliyense payekha amene akufuna kuti adziwe zoona zenizeni zimene Mawu a Mulungu amanena.Akolose 1:9, 10; 2 Timoteyo 2:24, 25.