Pitani ku nkhani yake

Kodi Muli ndi Lamulo Loletsa Mavidiyo Ena, Mabuku Ena Ndiponso Nyimbo Zina?

Kodi Muli ndi Lamulo Loletsa Mavidiyo Ena, Mabuku Ena Ndiponso Nyimbo Zina?

Ayi. Gulu lathu silinaike lamulo loletsa mafilimu, mabuku kapena nyimbo, zimene anthu a m’chipembedzochi ayenera kupewa. N’chifukwa chiyani zili choncho?

Baibulo limalimbikitsa munthu aliyense kuti aphunzitse ‘mphamvu zake za kuzindikira’ kuti azisiyanitsa choyenera ndi chosayenera.—Aheberi 5:14.

Malemba amapereka mfundo zimene Mkhristu angaziganizire akafuna kusankha zosangalatsa. * Pamoyo wathu wa tsiku ndi tsiku, timayesetsa ‘nthawi zonse kutsimikiza kuti chovomerezeka kwa Ambuye n’chiti.’—Aefeso 5:10.

Baibulo limaphunzitsa kuti bambo yemwe ndi mutu wa banja ali ndi udindo woyang’anira banja lake. Choncho akhoza kusankha kuti anthu a m’banja mwake asamaonere mavidiyo ena, asamawerenge mabuku ena ndiponso asamamvetsere nyimbo zina. (1 Akorinto 11:3; Aefeso 6:1-4) Koma palibe munthu amene ali ndi udindo wosankhira anthu a mu mpingo zinthu zina zosangalatsa zimene sayenera kuonera kapena kumvera.—Agalatiya 6:5.

^ ndime 4 Mwachitsanzo, Baibulo limaletsa chinthu chilichonse chimene chimalimbikitsa chiwawa, zamizimu kapena zachiwerewere.—Deuteronomo 18:10-13; Aefeso 5:3; Akolose 3:8.