Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

Kodi a Mboni za Yehova Amakhulupirira Zotani pa Nkhani ya Mwambo wa Maliro?

Kodi a Mboni za Yehova Amakhulupirira Zotani pa Nkhani ya Mwambo wa Maliro?

Timayesetsa kutsatira zimene Baibulo limaphunzitsa tikamachita mwambo wa maliro. Zina mwa zinthuzi ndi izi:

  • Si kulakwa kumva chisoni munthu amene timamukonda akamwalira. Ophunzira a Yesu analira anthu omwe ankawakonda atamwalira. (Yohane 11:33-35, 38; Machitidwe 8:2; 9:39) Choncho sitiona nthawi ya maliro ngati nthawi yosangalala. (Mlaliki 3:1, 4; 7:1-4) Koma timaona kuti ndi nthawi yachisoni.​—Aroma 12:15.

  • Akufa sadziwa kanthu. Ambonife timakhala m’mayiko osiyanasiyana komanso tili ndi zikhalidwe zosiyanasiyana. Komabe tonse timapewa kuchita zinthu zosonyeza kuti akufa amadziwa zimene zikuchitika. Sitikhulupiriranso kuti akufa amachita zinthu zomwe zingakhudze anthu a moyo. Timapewa zikhulupiriro zimenezi chifukwa ndi zosemphana ndi mfundo za m’Baibulo. (Mlaliki 9:5, 6, 10) Sitichitanso miyambo monga, kulondera maliro, kuchita phwando la maliro ndi kukumbukira tsiku limene munthu anamwalira, kupereka nsembe kwa akufa, kuyesa kulankhula ndi kupempha thandizo kwa akufa ndiponso kulowa chokolo. Timapewa miyambo imeneyi chifukwa choti timamvera lamulo la m’Baibulo lakuti: “Choncho tulukani pakati pawo . . . musakhudze chinthu chodetsedwa.” (2 Akorinto 6:17).

  • Anthu amene anamwalira adzakhalanso ndi moyo. Baibulo limanena kuti anthu amene anamwalira adzakhalanso ndi moyo ndipo imfa sidzakhalaponso. (Machitidwe 24:15; Chivumbulutso 21:4) Zimenezi zimatithandiza kuti tizipewa kumva chisoni mopitirira malire. Zimatithandizanso kuti tikamalira, tizilira mwa chiyembekezo ngati mmene Akhristu akale ankachitira.​—1 Atesalonika 4:13.

  • Baibulo limati tizichita zinthu mosapitirira malire. (Miyambo 11:2) Timakhulupirira kuti nthawi ya maliro si nthawi ‘yodzionetsera’ ndi zinthu zimene tili nazo. (1 Yohane 2:16) Timapewa kuchita miyambo yongofuna kusangalatsa anthu kapena kugula bokosi lodula kwambiri ndiponso kuvala zovala zapamwamba n’cholinga chogometsa anthu.

  • Sitikakamiza anthu ena kuti azitsatira zimene ifeyo timakhulupirira pa nkhani yokhudza mwambo wa maliro. Timachita zimenezi chifukwa timatsatira mfundo ya m’Baibulo yakuti: “Aliyense wa ife adzayankha yekha kwa Mulungu.” (Aroma 14:12) Koma anthu akafunsa zimene timakhulupirira, timayesetsa kuwafotokozera ndi “mtima wofatsa ndiponso mwaulemu kwambiri.”—1 Petulo 3:15.

Kodi n’chiyani chimachitika pamaliro a Mboni za Yehova?

Malo: Banja loferedwa ndi limene limasankha malo ochitira mwambo wa maliro. Ena angasankhe ku Nyumba ya Ufumu, kunyumba kwawo, malo otenthera mitembo kapena kumanda.

Mwambo wa maliro: Pamwambowu pamakambidwa nkhani yofotokoza zimene Baibulo limanena zokhudza imfa komanso zoti akufa adzauka. (Yohane 11:25; Aroma 5:12; 2 Petulo 3:13) Wokamba nkhaniyi angafotokozenso makhalidwe abwino amene munthu womwalirayo anali nawo komanso zimene anthu ena angaphunzirepo.—2 Samueli 1:17-27.

Pamwambowu pangaimbidwenso nyimbo yochokera M’malemba. (Akolose 3:16) Mwambowu umatha ndi pemphero lotonthoza.​—Afilipi 4:6, 7.

Malipiro: Sitimauza anamfedwa kuti apereke ndalama zolipirira wokamba nkhani ya maliro. Komanso mofanana ndi mmene timachitira pamisonkhano yathu, sitiyendetsa mbale ya zopereka pamwambo wamaliro.​—Mateyu 10:8.

Anthu oyenera kupezekapo: Mofanana ndi mmene zimakhalira ndi misonkhano yathu, anthu onse ngakhale omwe si a Mboni ndi olandiridwa pamwambo wa maliro womwe umachitikira ku Nyumba ya Ufumu.

Kodi a Mboni amapita kumwambo wa maliro wa zipembedzo zina?

Wa Mboni aliyense amasankha yekha zochita pa nkhaniyi, mogwirizana ndi zimene anaphunzira m’Baibulo. (1 Timoteyo 1:19) Komabe sitichita nawo miyambo ya maliro imene tikudziwa kuti sigwirizana ndi zimene Baibulo limanena.​—2 Akorinto 6:14-17.