Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kodi a Mboni za Yehova Amakakamiza Anthu Kuti Asinthe Zipembedzo Zawo?

Kodi a Mboni za Yehova Amakakamiza Anthu Kuti Asinthe Zipembedzo Zawo?

Ayi, ife sitichita zimenezo. Tinalemba m’magazini ina ya Nsanja ya Olonda kuti: “Kuumiriza anthu kuti asinthe chipembedzo chawo n’kulakwa.” a Sitikakamiza anthu kusintha zipembedzo zawo pa zifukwa izi:

  • Yesu sankakakamiza anthu kutsatira zimene ankaphunzitsa. Iye ankadziwa kuti ndi anthu ochepa okha amene angamvetsere ndi kugwiritsa ntchito uthenga wake. (Mateyu 7:13, 14) Nthawi ina pamene ophunzira ake ena anakhumudwa chifukwa cha zimene ankaphunzitsa, iye anawalola kumusiya ndipo sanawaumirize kuti azimutsatira.​—Yohane 6:​60-​62, 66-​68.

  • Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti asamakakamize anthu kusintha zimene amakhulupirira. M’malo mokakamiza anthu kuti azimvetsera uthenga wa Ufumu umene ankalalikira, ophunzira ake ankayenera kufufuza anthu omwe ankafunadi kumvetsera.​—Mateyu 10:7, 11-14.

  • Kukakamiza anthu kusintha zipembedzo zawo n’kosathandiza chifukwa Mulungu amafuna kuti anthu azimulambira ndi mtima wonse osati mochita kukakamizidwa.​—Deuteronomo 6:4, 5; Mateyu 22:37, 38.

Kodi timalalikira n’cholinga chofuna kukopa anthu?

N’zoona kuti timalalikira uthenga wa m’Baibulo “mpaka kumalekezero a dziko lapansi,” ndipo timafikira anthu “kunyumba ndi nyumba” mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena. (Machitidwe 1:8; 10:42; 20:20) Koma anthu ambiri amanena kuti timalalikira n’cholinga chofuna kukopa anthu ndipo Akhristu oyambirira ankanenedwanso zomwezi. (Machitidwe 18:12, 13) Kunena zoona limeneli ndi bodza lankunkhuniza. Ife sitikakamiza anthu kuti azikhulupirira zimene timaphunzitsa. M’malomwake, timafuna kuti anthu aziphunzira kaye n’cholinga choti asankhe okha zimene akufuna kukhulupirira.

Sitiumiriza anthu kuti asinthe zipembedzo zawo ndipo sitilowerera ndale pofuna kukwaniritsa zofuna za chipembedzo chathu. Sitipatsanso anthu zinthu n’cholinga chowakopa kuti alowe m’chipembedzo chathu. Zimenezi ndi zimene matchalitchi amene amati ndi achikhristu amachita koma n’zosemphana ndi zimene Yesu ankaphunzitsa. b

Kodi munthu ali ndi ufulu wosintha chipembedzo chake?

Mneneri Abulahamu anasiya chipembedzo cha makolo ake

Inde, chifukwa Baibulo limasonyeza kuti anthu ali ndi ufulu wosintha chipembedzo. M’Baibulo muli zitsanzo zambirimbiri za anthu amene anasintha chipembedzo cha makolo awo ndipo mwakufuna kwawo anayamba kutumikira Mulungu woona. Ena mwa anthuwa ndi Abulahamu, Rute, mtumwi Paulo ndiponso anthu ena a ku Atene. (Yoswa 24:2; Rute 1:14-16; Machitidwe 17:22, 30-34; Agalatiya 1:14, 23) Komanso Baibulo limasonyeza kuti anthu ena anasiya kulambira Mulungu mwakufuna kwawo ngakhale kuti kuchita zimenezi kunali kupanda nzeru.​—1 Yohane 2:19.

Munthu aliyense ali ndi ufulu wosintha chipembedzo ndipo zimenezi zilinso m’Chikalata cha Mfundo za Ufulu Wachibadwidwe cha bungwe la United Nations. Bungwe limati chikalatachi ndi ‘maziko a lamulo la padziko lonse lokhudza ufulu wachibadwidwe.’ Chikalatachi chimanena kuti munthu aliyense ali ndi ufulu wosintha chipembedzo kapena zimene amakhulupirira. Alinso ndi ufulu wofufuza, kumva komanso kuuza ena mfundo zosiyanasiyana, zomwe zikuphatikizapo mfundo zachipembedzo. c Ngakhale kuti chikalatachi chinanena zimenezi, munthu amafunika kulemekezanso ufulu wa ena wochita zimene amakhulupirira ndiponso wosatsatira mfundo zachipembedzo zimene sagwirizana nazo.

Kodi munthu akalowa chipembedzo china ndiye kuti sanalemekeze makolo ake ?

Ayi si choncho. Baibulo limatilimbikitsa kuti tiyenera kulemekeza munthu aliyense mosatengera chipembedzo chake. (1 Petulo 2:17) Kuwonjezera pamenepa, a Mboni za Yehova amamvera lamulo la m’Baibulo lolemekeza makolo awo ngakhale zitakhala kuti amakhulupirira zosiyana.​—Aefeso 6:2, 3.

Komabe si onse amene amagwirizana ndi zimene Baibulo limanena. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi zimene zinachitikira mayi wina amene anakulira m’dziko la Zambia. Iye ananena kuti: “M’dera lakwathu, munthu akasintha chipembedzo chake anthu amamuona kuti sakulemekeza makolo ake ndiponso anthu a m’mudzi wake.” Mayiyu anakumana ndi zimenezi ali wachinyamata pa nthawi yomwe ankaphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova ndiponso ataganiza kuti asinthe chipembedzo. Iye anapitiriza kunena kuti: “Makolo anga ankandiuza mobwerezabwereza kuti ndikuwakhumudwitsa. Zimenezi zinali zovuta kwa ine chifukwa sindinkafuna kuti makolo anga azikhumudwa chifukwa cha zochita zanga.  . . Koma ndinaona kuti ndiyenera kukhala wokhulupirika kwa Yehova m’malo motsatira miyambo ya chipembedzo ndipo zimenezi sizinatanthauze kuti sindikonda makolo anga.” d

a Onani Nsanja ya Olonda ya January 1, 2002, tsamba 12 ndime 15.

b Mwachitsanzo, cha m’ma 785 C.E., mfumu ina m’dera la Saxony dzina lake Charlemagne inalamula kuti munthu aliyense amene sabatizidwa kuti akhale Mkhristu aphedwa. Chikalata cha mgwirizano wa mtendere chimene chinasainidwa mu Ufumu wa Roma mu 1555 C.E. pakati pa magulu amene ankakangana, chinanena kuti aliyense amene akulamulira kachigawo ka ufumuwu ayenera kukhala wa chipembedzo cha Katolika kapena Lutheran. Chikalatacho chinawonjezera kuti aliyense ayenera kulowa chipembedzo cha amene akulamulira pa nthawiyo ndipo amene wakana ayenera kuchoka m’dzikolo.

c Maufulu ngati amenewa akupezekanso mu African Charter on Human and Peoples’ Rights, American Declaration of the Rights and Duties of Man, 2004 Arab Charter on Human Rights, Association of Southeast Asian Nations ndi mu Pangano la Dziko Lonse la Ufulu wa Anthu ndi wa Zandale. Komabe mayiko amene anavomereza mapangano amenewa amachita zosiyanasiyana potsatira maufulu amenewa.

d Yehova ndi dzina la Mulungu lomwe limapezeka m’Baibulo.