Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

Kodi Mumapewa Anthu Amene Kale Anali M’chipembedzo Chanu?

Kodi Mumapewa Anthu Amene Kale Anali M’chipembedzo Chanu?

Ife sitipewa anthu amene anabatizidwa kukhala a Mboni za Yehova koma tsopano sakugwiranso ntchito yolalikira, kapena asiyiratu kusonkhana nafe. M’malomwake, timayesetsa kufufuza anthu oterewa kuti tiwathandize n’cholinga choti ayambirenso kukonda Mulungu.

Komanso sikuti timangofikira kuchotsa mumpingo munthu yemwe wachita tchimo lalikulu. Komabe, ngati wa Mboni wobatizidwa akupitiriza kuphwanya mfundo za m’Baibulo ndipo sakulapa, amachotsedwa mumpingo ndipo timamupewa. Baibulo limanena momveka bwino pa nkhaniyi kuti: “M’chotseni pakati panu munthu woipayo.”—1 Akorinto 5:13.

Nanga zimakhala bwanji ngati munthu yemwe wachotsedwa mumpingoyo ndi bambo koma mkazi ndi ana ake adakali a Mboni za Yehova? Chibale cha anthuwo sichitha, koma anthu a Mboniwo amangosintha mmene amachitira zinthu zokhudzana ndi chipembedzo ndi bamboyo. Choncho mkazi ndi anawo amapitiriza kuchitira pamodzi zinthu zatsiku ndi tsiku zokhudza moyo wawo wa banja ndi bamboyo.

Komanso anthu amene anachotsedwa amakhoza kumapezeka pamisonkhano yathu. Ngati anthuwo akufuna, amathanso kupatsidwa malangizo a m’Baibulo ndi akulu a mumpingo. Cholinga chimakhala chofuna kuthandiza munthuyo kuti asinthe n’kukhalanso wa Mboni za Yehova. Anthu amene anachotsedwa mumpingo, omwe asiya khalidwe lawo loipa ndipo akusonyeza kuti akufunitsitsa kuyambiranso kutsatira mfundo za m’Baibulo pa moyo wawo, amaloledwa kubwereranso mumpingo ndipo amalandiridwa ndi manja awiri.