Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

Kodi Mumakhulupirira Kuti Dziko Linalengedwa M’masiku 6 Enieni?

Kodi Mumakhulupirira Kuti Dziko Linalengedwa M’masiku 6 Enieni?

Ayi. N’zoona kuti a Mboni za Yehova amakhulupirira kuti Mulungu analenga zinthu zonse. Koma sitikhulupirira kuti Mulungu analenga zinthu zonse m’masiku 6 enieni chifukwa zinthu zina zokhudza chikhulupirirochi ndi zosemphana ndi zimene Baibulo limanena. Taonani zitsanzo zotsatirazi:

  1. Kutalika kwa masiku 6 amene Mulungu analenga zinthu zonse. Anthu ena amakhulupirira kuti Mulungu analenga zinthu zonse m’masiku 6 enieni, tsiku lililonse lokhala ndi maola 24. Koma m’Baibulo, mawu akuti “tsiku” akhoza kutanthauza nthawi yaitali.Genesis 2:4; Salimo 90:4.

  2. Kodi dzikoli lakhalapo kwa zaka zingati? Anthu ena amaphunzitsa kuti dzikoli langokhala zaka masauzande ochepa kuchokera nthawi imene linalengedwa. Komabe Baibulo limasonyeza kuti dziko lapansili komanso chilengedwe chonse zinalipo masiku 6 olenga amene amatchulidwa m’Baibulo asanafike. (Genesis 1:1) Pa chifukwa chimenechi, a Mboni za Yehova satsutsa zimene asayansi ena apeza, zoti dziko lapansili lakhalapo zaka mabiliyoni ambiri kuchokera nthawi imene linalengedwa.

Ngakhale kuti a Mboni za Yehovafe timakhulupirira kuti dzikoli linalengedwa ndi Mulungu, sititsutsa zimene asayansi ena amapeza. Timakhulupirira kuti zinthu zolondola zimene asayansi angapeze zimagwirizana ndi zimene Baibulo limanena.

 

Onaninso

Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?

Baibulo Ndi Buku Lochokera Kwa Mulungu

Kodi Baibulo lingakuthandizeni bwanji kupirira mavuto anu? N’chifukwa chiyani muyenera kukhulupirira maulosi a m’Baibulo?

GALAMUKANI!

Kodi Baibulo Limanena Zotani Zokhudza Chilengedwe?

Baibulo limafotokoza za masiku 6 amene Mulungu analenga zinthu. Kodi masiku amenewa anali a maola 24?

KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO

Kodi Sayansi Imagwirizana ndi Baibulo?

Kodi m’Baibulo muli mfundo zolakwika zokhudza sayansi?