Pitani ku nkhani yake

Kodi Phunziro la Baibulo N’chiyani?

Kodi Phunziro la Baibulo N’chiyani?

A Mboni za Yehova amachita maphunziro a Baibulo ndi anthu, ndipo amathandiza anthuwo, kudziwa mayankho a mafunso osiyanasiyana, monga awa:

  • Kodi Mulungu ndani?

  • Kodi Mulungu amandiwerengera?

  • Kodi ndingatani kuti banja langa liziyenda bwino?

  • Kodi ndingatani kuti ndikhale ndi moyo wosangalala?

M’munsimu muli mayankho a mafunso amene anthu amafunsa kawirikawiri, okhudza phunziro la Baibulo.

Kodi phunziro la Baibulo limayenda bwanji? Timasankha mitu yosiyanasiyana, monga mutu wakuti “Mulungu” kapena “ukwati,” kenako n’kukambirana malemba osiyanasiyana a m’Baibulo ogwirizana ndi mutuwo. Timayerekezera mavesiwo kuti tidziwe zimene Baibulo lonse limanena pa nkhaniyo, ndipo mwanjira imeneyi, timalola kuti Baibulo lizizitanthauzira lokha.

Kuti tiphunzire Baibulo mosavuta, timagwiritsa ntchito buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Bukuli limafotokoza momveka bwino zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhani zosiyanasiyana, monga zokhudza Mulungu, Yesu ndiponso tsogolo lathu.

Kodi ndiyenera kupereka ndalama kuti ndiziphunzira Baibulo? Ayi. Phunziroli ndi laulere, ndipo mabuku amene timagwiritsa ntchito pophunzira alibe mtengo.

Kodi phunziro la Baibulo limatenga nthawi yaitali bwanji ulendo uliwonse? Anthu ambiri amasankha kuti tizichita nawo phunziro la Baibulo pafupifupi kwa ola limodzi mlungu uliwonse. Komabe, kutalika kwa nthawi ya phunziroli kumasiyanasiyana malinga ndi mmene zinthu zilili. Ifeyo timavomereza kusintha kuti tigwirizane ndi zimene inuyo mukufuna.

Kodi chimachitika n’chiyani munthu akapempha kuti aziphunzira Baibulo? Mukapempha phunziro la Baibulo, munthu wa Mboni za Yehova adzabwera kuti aonane nanu pa nthawi ndi malo amene inuyo mungakonde. Kwa nthawi yochepa, iye adzakusonyezani mmene phunziroli limachitikira. Zikatero, mukhoza kupitiriza kuphunzira ngati mungakonde.

Ngati nditavomereza kuti ndiziphunzira Baibulo, kodi ndiyenera kulowa chipembedzo cha Mboni za Yehova? Ayi, ndithu. Ifeyo timasangalala kuphunzitsa anthu Baibulo, koma sitikakamiza anthu kuti alowe chipembedzo chathu. M’malomwake, timawafotokozera mwaulemu zimene Baibulo limanena, ndipo timazindikira kuti munthu aliyense ali ndi ufulu wosankha zimene akufuna kuti azikhulupirira.—1 Petulo 3:15.