Pitani ku nkhani yake

Kodi a Mboni za Yehova ndi a Mpatuko?

Kodi a Mboni za Yehova ndi a Mpatuko?

Ayi, a Mboni za Yehova si gulu la mpatuko. M’malomwake, ndife Akhristu ndipo timayesetsa kutsanzira chitsanzo cha Yesu Khristu komanso kuchita zimene iye anatiphunzitsa.

Kodi mawu akuti mpatuko amatanthauza chiyani?

Anthu amatanthauzira mawu akuti “mpatuko” mosiyanasiyana. Komabe, m’nkhaniyi tiona zinthu ziwiri zimene anthu ambiri amaganiza akamva mawuwa. Tionanso kusiyana kwa zinthu zimenezi ndi mmene ifeyo tilili.

  • Ena amaganiza kuti a mpatuko ndi gulu logalukira ku chipembedzo china n’kuyambitsa chawo. A Mboni za Yehova sanayambitse chipembedzo chatsopano. M’malomwake, timalambira mofanana ndi mmene Akhristu oyambirira ankachitira, ndipo zimene ankachita komanso zimene ankaphunzitsa zinalembedwa m’Baibulo. (2 Timoteyo 3:16, 17) Timakhulupirira kuti anthu ayenera kutsatira zimene Malemba Opatulika amanena pa nkhani yokhudza kulambira.

  • Anthu ena akamva za mpatuko amaganiza za gulu loopsa lachipembedzo lokhala ndi munthu wolitsogolera. A Mboni za Yehova alibe munthu amene amamuona kuti ndi mtsogoleri wawo. M’malomwake, timatsatira zimene Yesu anauza ophunzira ake pamene ananena kuti: “Mtsogoleri wanu ndi mmodzi, Khristu.”Mateyu 23:10.

A Mboni za Yehova si gulu loopsa la mpatuko. Iwo amachita zinthu zimene zimathandiza anthu a m’chipembedzo chawo komanso anthu a m’dera limene akukhala. Mwachitsanzo, ntchito yathu yolalikira yathandiza anthu ambiri kusiya makhalidwe oipa, monga kugwiritsira ntchito mankhwala osokoneza bongo komanso kumwa mowa mwauchidakwa. Kuwonjezera pamenepa, padziko lonse lapansi timathandiza anthu ambirimbiri kuphunzira kuwerenga ndi kulemba. Komanso timathandiza pakagwa masoka a chilengedwe. Timagwira ntchito mwakhama pothandiza ena, ndipo izi n’zimene Yesu analamula otsatira ake kuti azichita.Mateyu 5:13-16.