Pitani ku nkhani yake

Kodi Mumakhulupirira Yesu?

Kodi Mumakhulupirira Yesu?

Inde. Timakhulupirira Yesu amene anati: “Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.” (Yohane 14:6) Timakhulupirira kuti Yesu anabwera padziko lapansi kudzapereka moyo wake wangwiro monga nsembe yowombola anthu. (Mateyu 20:28) Chifukwa chakuti iye anafa komanso kuukitsidwa, zimakhala zotheka kuti anthu amene amamukhulupirira adzapeze moyo wosatha. (Yohane 3:16) Timakhulupiriranso kuti panopa Yesu akulamulira monga Mfumu mu Ufumu wakumwa wa Mulungu, umene posachedwapa udzabweretsa mtendere padziko lonse lapansi. (Chivumbulutso 11:15) Komabe, timaona Yesu mogwirizana ndi zimene iyeyo ananena pamene anati: “Atate ndi wamkulu kuposa ine.” (Yohane 14:28) Choncho sitilambira Yesu popeza timadziwa kuti iyeyo si Mulungu Wamphamvuyonse.