Pitani ku nkhani yake

N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Anasintha Zinthu Zina Zomwe Ankakhulupirira?

N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Anasintha Zinthu Zina Zomwe Ankakhulupirira?

Zonse zimene timakhulupirira zimachokera m’Baibulo. Choncho tinasintha zinthu zina zomwe tinkakhulupirira chifukwa chomvetsa bwino mfundo za m’Malemba. *

Zimenezi n’zogwirizana kwambiri ndi mfundo ya pa Miyambo 4:18, yomwe imati: “Koma njira ya olungama ili ngati kuwala kwamphamvu kumene kumamka kuwonjezereka mpaka tsiku litakhazikika.” Dzuwa likamatuluka limayamba kuwala pang’onopang’ono ndipo timayamba kuona bwino zinthu, mofanana ndi zimenezi Mulungu amatithandiza kumvetsa bwino mfundo za m’Mawu ake pang’onopang’ono komanso pa nthawi yake. (1 Petulo 1:10-12) Ndipo monga mmene Baibulo linaneneratu, Yehova wathandiza anthu kuti azimvetsa Mawu ake mofulumira kwambiri “nthawi yamapeto” ino.​—Danieli 12:4.

Choncho, tisamadabwe kapena kukhumudwa zinthu zimene timakhulupirira zikasintha. Tikutero chifukwa chakuti atumiki a Mulungu akale nawo ankafunikanso kusintha zinthu zina zomwe poyamba ankazikhulupirira komanso kuziyembekezera.

  • Mose ali ndi zaka 40 ankafuna kupulumutsa mtundu wa Isiraeli koma nthawi yoti Mulungu achite zimenezi inali isanakwane.​—Machitidwe 7:23-25, 30, 35.

  • Atumwi sanamvetse ulosi womwe unkanena za kuphedwa kwa Mesiya komanso kuukitsidwa kwake.​—Yesaya 53:8-12; Mateyu 16:21-23.

  • Akhristu ena akale anali ndi maganizo olakwika okhudza nthawi imene“tsiku la Yehova” lidzafike.—2 Atesalonika 2:1, 2.

Komabe patapita nthawi, Mulungu anawathandiza kumvetsa zinthu zimene sankazimvetsa. Ifenso timapempha Mulungu kuti apitirize kutithandiza kumvetsa bwino Mawu ake.​—Yakobo 1:5.

^ ndime 2 Tikamvetsa bwino mfundo zina za m’Baibulo, timasintha ndipo sitibisa. Koma timazilemba n’kuzifalitsa kuti anthu adziwe. Mwachitsanzo, mungafufuze mawu akuti “Beliefs Clarified” pawebusaiti yathu yachingelezi.