Pitani ku nkhani yake

Kodi a Mboni za Yehova Amatsatira Mfundo Ziti Zokhudza Kukhala pa Chibwenzi?

Kodi a Mboni za Yehova Amatsatira Mfundo Ziti Zokhudza Kukhala pa Chibwenzi?

A Mboni za Yehova amakhulupirira kuti mfundo ndiponso malamulo a m’Baibulo angatithandize kuti tizisankha zochita mwanzeru komanso tizisangalatsa Mulungu. (Yesaya 48:17, 18) Sikuti tinakhazikitsa mfundo ndiponso malamulowa koma timayesetsa kuwatsatira. Tiyeni tione malamulo ndiponso mfundo zina za m’Baibulo zokhudza chibwenzi. *

  • Anthu amene akwatirana sayenera kusiyana. (Mateyu 19:6) Ndiyeno a Mboni za Yehova amaona kuti anthu ayenera kukhala pa chibwenzi pokhapokha ngati ali ndi cholinga choti adzakwatirane. Choncho amaona kuti kukhala pa chibwenzi ndi nkhani yaikulu.

  • Anthu amene ayenera kukhala pa chibwenzi ayenera kukhala okhawo amene akula n’kufika poti akhoza kukhala pa banja. Anthuwa ayenera kukhala oti ‘apitirira pachimake pa unyamata,’ kapena kuti adutsa msinkhu womwe chilakolako cha kugonana chimakhala champhamvu.—1 Akorinto 7:36.

  • Anthu amene ali pa chibwenzi ayenera kukhala anthu amene sali kale pa banja. Mulungu amaona kuti anthu ena amene anathetsa banja lawo kukhoti adakali pa banja. Zili choncho chifukwa chakuti Mulungu amaona kuti banja likhoza kutha pokhapokha ngati wina wachita dama.—Mateyu 19:9.

  • Mkhristu amene akufuna kukhala pa banja ayenera kusankha munthu yemwe ndi Mkhristu mnzake. (1 Akorinto 7:39) A Mboni za Yehova amaona kuti lamuloli silikungonena za munthu amene amalemekeza zimene timakhulupirira koma amatsatira zinthuzo ndipo ndi wa Mboni wobatizidwa. (2 Akorinto 6:14) Kuyambira kale, Mulungu wakhala akuuza atumiki ake kuti azikwatirana ndi okhawo amene amakhulupirira zimene iwowo amakhulupirira. (Genesis 24:3; Malaki 2:11) Akatswiri pa nkhani ya banja aona kuti zimenezi n’zothandiza. *

  • Ana ayenera kumvera makolo awo. (Miyambo 1:8; Akolose 3:20) Ana amene adakali pakhomo pa makolo awo ayenera kumvera malamulo a makolowo pa nkhani ya chibwenzi. Malamulowo angakhudze msinkhu umene anawo angakhale pa chibwenzi komanso zimene sayenera kuchita akakhala pa chibwenzicho.

  • Wa Mboni aliyense amasankha yekha pa nkhani ya kukhala pa chibwenzi komanso munthu amene angakhale naye pa chibwenzicho. Koma pochita zimenezi amatsatira mfundo za m’Baibulo. Izi zikugwirizana ndi mfundo yakuti: “Aliyense ayenera kunyamula katundu wake.” (Agalatiya 6:5) Komabe a Mboni ambiri amene akufuna kukhala pa chibwenzi amafunsira nzeru kwa a Mboni achikulire omwe amawafunira zabwino.—Miyambo 1:5.

  • Zinthu zambiri zimene anthu amachita akakhala pa chibwenzi ndi machimo akuluakulu. Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti tiyenera kupewa kuchita dama. Dama limatanthauza kugonana komanso zinthu zina monga kuseweretsa maliseche a munthu amene si mwamuna kapena mkazi wako komanso kugonana m’kamwa kapena kumatako. (1 Akorinto 6:9-11) Anthu ena akakhala pa chibwenzi amagwiranagwirana komanso kuchita zinthu zina zodzutsa chilakolako chogonana ngakhale kuti safika pogonana. Mulungu amaona kuti anthuwa akuchita “zinthu zodetsa.” (Agalatiya 5:19-21) Baibulo limaletsanso kukambirana “nkhani zotukwana” zokhudza kugonana.—Akolose 3:8.

  • Mtima, womwe ndi munthu wamkati, ndi wonyenga. (Yeremiya 17:9) Mtima ungachititse munthu kuchita zinthu zimene akudziwa kuti ndi zoipa. Choncho anthu amene ali pa chibwenzi angachite bwino kupewa kukhala okhaokha pamalo amene palibe anthu ena amene akuwaona. Iwo angasankhe kuti nthawi zonse akhale pa gulu kapena limodzi ndi munthu wina wamkulu. (Miyambo 28:26) Akhristu amene akufuna kukhala pa banja amazindikira kuti si bwino kungoyamba chibwenzi pa Intaneti ndi munthu amene sakumudziwa kwenikweni.—Salimo 26:4.

^ ndime 2 Anthu a zikhalidwe zina sakhala pa chibwenzi asanakwatirane. Baibulo silinena kuti anthu ayenera kukhala kaye pa chibwenzi kuti akwatirane.

^ ndime 6 Mwachitsanzo, nkhani ina m’magazini ina yokhudza banja inati: “Anthu ena anapanga kafukufuku maulendo atatu ndipo anapeza kuti anthu ambiri amene akhala pa banja nthawi yaitali (zaka 25 mpaka 50 kapena zoposa) ndi amene ali m’chipembedzo chimodzi ndipo amakhulupirira zofanana.”—Marriage & Family Review, Voliyumu 38, magazini yoyamba, tsamba 88 (2005).