Pitani ku nkhani yake

N’chifukwa Chiyani Mumati Ndinu Mboni za Yehova?

N’chifukwa Chiyani Mumati Ndinu Mboni za Yehova?

 Baibulo limati dzina la Mulungu ndi Yehova. (Ekisodo 6:3; Salimo 83:18) Mawu akuti mboni amatanthauza munthu amene amanena kapena kulengeza zinthu zimene akukhulupirira kuti ndi zoona.

 Choncho, dzina lathu lakuti Mboni za Yehova limasonyeza kuti ndife gulu la Akhristu amene amalengeza mfundo zoona zokhudza Yehova, Mlengi wa zinthu zonse. (Chivumbulutso 4:11) Timachitira umboni kwa anthu ena m’njira ziwiri. Njira yoyamba ndi mmene timachitira zinthu pa moyo wathu, ndipo njira yachiwiri timawauza zimene taphunzira m’Baibulo.—Yesaya 43:10-12; 1 Petulo 2:12