Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kodi a Mboni za Yehova Amagwiritsa Ntchito Bwanji Ndalama Zimene Anthu Amapereka?

Kodi a Mboni za Yehova Amagwiritsa Ntchito Bwanji Ndalama Zimene Anthu Amapereka?

 Timagwiritsa ntchito ndalama zimene anthu amapereka poyendetsa ntchito za gulu lathu zachipembedzo komanso zothandiza anthu. Timagwira ntchitozi pofuna kukwaniritsa ntchito yathu yaikulu yomwe ndi kuthandiza anthu kuti akhale ophunzira a Yesu Khristu.—Mateyu 28:19, 20.

 Sitigwiritsa ndalamazi pofuna kulemeretsa winawake. Tilibe akulu kapena atsogoleri amene amalipiridwa. Komanso a Mboni za Yehova salipiridwa kuti aziyenda kunyumba ndi nyumba. Anthu amene amagwira ntchito kumaofesi a nthambi kapena kulikulu lapadziko lonse, kuphatikizapo a m’Bungwe Lolamulira, salandira malipiro.

Ntchito Zathu Zina

  •   Kufalitsa Mabuku: Timamasulira, kusindikiza, kutumiza komanso kugawira Mabaibulo ndi mabuku ena a Chikhristu mamiliyoni ambiri chaka chilichonse kwaulere. Webusaiti yathu ya jw.org komanso pulogalamu ya JW Library zimathandiza anthu kuti azilandira mabuku athu pazipangizo zawo kwaulere komanso popanda kutsatsa malonda.

  •   Kumanga ndi Kukonza Nyumba: Timamanga komanso kukonza nyumba zolambirira padziko lonse lapansi n’cholinga choti mipingo yathu izikhala ndi malo olemekezeka oti izisonkhanamo n’kutamanda Mulungu. Timamanganso ndi kukonza maofesi a nthambi ndiponso omasulira mabuku. Ntchito zambiri zimagwiridwa ndi anthu ongodzipereka zomwe zimathandiza kuti tisamawononge ndalama zambiri.

  •   Kuyang’anira: Ntchito zonse kulikulu lathu lapadziko lonse, kumaofesi a nthambi ndi kumaofesi omasulira mabuku komanso ntchito za oyang’anira oyendayenda, zimayendetsedwa ndi ndalama zimene anthu amapereka pothandiza ntchito zathu zapadziko lonse.

  •   Kulalikira: A Mboni salipiridwa kuti azilalikira uthenga wabwino kapena kuti aziphunzitsa anthu “mawu a Mulungu.” (2 Akorinto 2:17) Koma pali a Mboni ena osankhidwa komanso ophunzitsidwa amene amagwiritsa ntchito nthawi yawo yambiri pothandiza pa ntchito yolalikira. Ndipo mofanana ndi mmene zinalili ndi Akhristu oyambirira, iwo amapatsidwa malo okhala komanso zofunika pa moyo.—Afilipi 4:16, 17; 1 Timoteyo 5:17, 18.

  •   Kuphunzitsa: Ndalama zimene timagwiritsa ntchito popanga misonkhano yathu ikuluikulu zimachokera kwa anthu amene amazipereka mwa kufuna kwawo. Timagwiritsanso ntchito ndalamazi popanga mavidiyo komanso zinthu zongomvetsera zophunzitsa Baibulo. Komanso timapanga masukulu ophunzitsira akulu ndi atumiki a nthawi zonse kuti azigwira bwino ntchito zawo.

  •   Kuthandiza Pakachitika Ngozi: Timapereka chakudya, madzi ndi pokhala kwa anthu amene akhudzidwa ndi ngozi zachilengedwe kapena ngozi zina. Ntchito imeneyi imathandiza “abale ndi alongo athu m’chikhulupiriro” komanso anthu ena amene si Mboni.—Agalatiya 6:10.