ONANI

Pangani Dawunilodi:

 1. 1. Moyo ndi wovutadi lero

  Tingafo’ke ndi zomwe zikuchitika.

  Anzathu angatikhumudwitse.

  Pemphera kwa Yehova

  Chamumtima.

  (KOLASI)

  ’Sagonje; pilira.

  Udalire Yehova.

  Zidzatiyendera

  Tikamapemphera.

  Zinthu zikavuta,

  Iye adzatithandiza.

  Ndi m’busa wathu, wabwino

  Tikamamupempha.

  Amamvetsera.

  Mosangalala.

 2. 2. Mavuto azachuma nawo.

  Angatichititse kusasangalala.

  Komabe timapeza chimwemwe

  Tikathandiza ena

  Kusangalala.

  (KOLASI)

  Usakayikire.

  Udalire Yehova.

  Zidzatiyendera

  Tikamapemphera.

  Timapeza mphamvu.

  Podziwa atithandiza

  Ndi mbusa wathu wabwino

  Tikamamupempha

  Amamvetsera

  Mosangalala.

  (KOLASI)

  Udalire Yehova.

  Zidzakuyendera

  Ukamapemphera.

  Timapeza mphamvu.

  Podziwa atithandiza.

  Ndi M’busa wathu wabwino.

  Tikamamupempha.

  Amamvetsera.

  Mosangalala.