ONANI

Pangani Dawunilodi:

 1. 1. Ndinangosiidwa,

  Ndili ndekhandekha,

  Ndilibiletu mzanga,

  Ndakhumudwatu kwambiri.

  Palibenso munthu,

  Wondilimbikitsa,

  Ndani anditonthoze?

  Ndani andilimbikitse?

  (KOLASI)

  Ali nane;

  Nthawi zonse.

  Muli monse,

  Sandisiya.

  Yehovatu,

  Amadziwa.

  Amayankha

  Mapemphero.

  M’mayesero onse,

  Sangandisiye.

 2. 2. N’ngasiye zambiri

  N’khale bwenzi lanu,

  Ena ‘ngandilakwire,

  Koma inu simusintha

  Mwandiyandikira,

  Mulidi pafupi.

  Ndimakudalirani​—

  Simungandikhumudwitse.

  (KOLASI)

  Ali nane;

  Nthawi zonse.

  Muli monse,

  Sandisiya.

  Yehovatu,

  Amadziwa.

  Amayankha

  Mapemphero.

  M’mayesero onse,

  Sangandisiye

  Nthawi zonse.

  Muli monse,

  Sandisiya.

  Yehovatu,

  Amadziwa.

  Amayankha

  Mapemphero.

  M’mayesero onse,

  Sangandisiye.