Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Nyimbo Zathu

Ndimasunga Malamulo Anu

Ndimasunga Malamulo Anu
ONANI
Kukula kwa Zilembo

Pangani Dawunilodi:

 1. 1. Ndingatani? N’dalire ndani?

  N’zabwinobwino, sizingandivulaze.

  Palibe vuto ngati n’tachita nawo.

  Koma chofunika n’chani? Njira ndi iti?

  Ndingatani? N’tsatire ziti?

  Kumwa kwambiri, ndi mavuto ena​—

  Ndingakumane ndi misampha yambiri.

  Kodi chofunika n’chani? Yehova chonde ndimvereni.

  (KOLASI)

  Malamulo anu, ndimawasunga.

  Ndipotu ndimawakonda nthawi zonse.

  Zomwe ndinamva m’mawu anu, mun’thandize kuzimvetsa.

 2. 2. Ndizofunikadi, ndikudalireni.

  Sindikufuna kuphwanya malamulo.

  Koma ndikudziwa izi sizophweka.

  Ndikudziwa zoyenera ndi​—⁠zoda-liri-kadi.

  (KOLASI)

  Malamulo anu, ndimawasunga.

  Amandilimbitsa mtima nthawi zonse.

  Zomwe ndinamva m’mawu anu, mun’thandize kuzimvetsa.

  (KOLASI)

  Malamulo anu, ndimawasunga.

  Amandilimbitsa mtima nthawi zonse.

  Pomwe ndikuwerenga nthawi zonse,

  M’mandiwunikira, M’makhala pambali panga.

  Zomwe ndinamva m’mawu anu, mundithandize ndimvetse.