Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndidzakupatsani Zonse Zomwe Ndingathe

Ndidzakupatsani Zonse Zomwe Ndingathe
ONANI

Pangani Dawunilodi:

 1. 1. Yehova n’kupatseni zonse zomwe ndingathe.

  Ndikufuna kukusangalatsani kwa moyo wonse.

  Ndidzathandiza ena kuti akudziweni.

  Ntchitoyi imandithandiza kusangalala.

  (VESI LOKOMETSERA)

  N’kamakutamandani ndimalimba nthawi zonse.

  Paja ndinalonjeza kukutumikirani.

  (KOLASI)

  Tate Yehova n’dzakutamandani,

  N’dzatumikiradi m’njira zambiri.

  Ndadzipereka moyo wanga wonse.

  Ndidzakupatsani zonse zo-mwe ndingathe.

 2. 2. Ndidzakonda Yehova ndi abale onse.

  Ndidziperekadi ndithu mmene ndingathere.

  Kupatsa ndi kwabwino kuposa kulandira,

  Choncho n’zithera nthawi yanga pothandiza ena.

  (VESI LOKOMETSERA)

  N’kamakutamandani ndimalimba nthawi zonse.

  Paja ndinalonjeza kukutumikirani.

  (KOLASI)

  Tate Yehova n’dzakutamandani,

  N’dzatumikiradi m’njira zambiri.

  Ndadzipereka moyo wanga wonse.

  Ndidzakupatsani zonse zo-mwe ndingathe.

  (KOLASI)

  Tate Yehova n’dzakutamandani,

  N’dzatumikiradi m’njira zambiri.

  Ndadzipereka moyo wanga wonse.

  Ndidzakupatsani zonse zo-mwe ndingathe.