ONANI

Pangani Dawunilodi:

 1. 1. Yendani m’sathamange.

  Inde mukusangalala.

  Koma pakakhala anthu,

  Simuyeneratu,

  Kuthamanga.

  (KOLASI)

  M’sathamange.

  Ndi bwinotu mufatse.

  Mudzapeza chimwemwe.

  M’sathamange.

 2. 2. Inde muli n’zochita

  Komanso anthu owathandiza

  Komatu m’saiwale.

  Muwasonyeze,

  Mumawakonda.

  (KOLASI)

  M’sathamange.

  Ndi bwinotu mufatse.

  Mudzapeza chimwemwe.

  M’sathamange.

 3. 3. Mungafulumire ndithu.

  Pokagogoda

  Khomo lamunthu

  N’kufufuza eni khomo

  Koma odutsa

  Chezani nawo.

  (KOLASI)

  M’sathamange.

  Ndi bwinotu mufatse.

  Mudzapeza chimwemwe.

  M’sathamange

  O. M’sathamange.