ONANI

Pangani Dawunilodi:

 1. 1. Nyimbo zisanayambepo kumveka,

  Anthu ’kubwera; anthu ’kudzadzadi.

  M’dzikoli anthu sagwirizana.

  Koma ife tili pamtendere.

  (KOLASI)

  Tili ngati pachibale timakondanadi.

  Ngakhale kuti ndi koyamba kuonanaku.

  Tili ngati pachibale timakondanadi.

  Ngakhale kuti ndi koyamba kuonanaku.

 2. 2. Ndikuona gulu lonseli pomwe ndakhala.

  Ndikungoona nkhope zosazidziwa.

  Ndife a m’banja; limodzidi.

  Munandibayibitsa m’sitediyamu.

  Zosangalatsa!

  Zinanditsitsimuladi ndithuu.

  Pang’onong’ono, n’kanalira.

  (KOLASI)

  Tili ngati pachibale, timakondanadi.

  Ngakhale kuti ndi koyamba kuonanaku.

  Tili ngati pachibale, timakondanadi.

  Ngakhale kuti ndi koyamba kuonanaku.

  (VESI LOKOMETSERA)

  Tigwirane.

  Mavuto n’ngofanana.

  Timalimba

  Poyang’ana pamoyo wosatha.

  (KOLASI)

  Tili ngati pachibale, timakondanadi.

  Ngakhale kuti ndi koyamba kuonanaku.

  Tili ngati pachibale, timakondanadi.

  Ngakhale kuti ndi koyamba kuonanaku.

  Ngakhale kuti ndi koyamba kuonanaku.