Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kungomwetulira

Kungomwetulira
ONANI

Pangani Dawunilodi:

 1. 1. Tinganenetu zambiri;

  Zosiyanasiyana;

  Tingajambule zithunzi,

  Komabe osasintha

  Tingayese kuwasintha

  M’mawu ndi m’zochitanso,

  Pena chofunika ndi

  Kungomwetulira.

  (KOLASI)

  Kungowamwetulira ndithu,

  Mudzapezadi poyambira.

  Mukapemphera mudzakwanitsa,

  Chofunika n’kungomwetulira.

 2. 2. Anthu ena ndi oipa—sachita chilungamo.

  Amachitanso zankhanza, anthu akuvutika.

  Timaona nkhope zawo, akamadutsa m’njira.

  Timawatonthoza n’kuwauza zam’tsogolo.

  (KOLASI)

  Kungowamwetulira ndithu,

  Mudzapezadi poyambira.

  Mukapemphera mudzakwanitsa,

  Chofunika n’kungomwetulira.

 3. 3. Pena timakhumudwa anthu akakana

  Uthenga wofunika womwe tikulengeza.

  Mitima ina n’njovuta kulandira uthenga.

  Nsangala n’kumwetulira, n’zomwe akufuna.

  (KOLASI)

  Kungowamwetulira ndithu,

  Mudzapezadi poyambira.

  Mukapemphera mudzakwanitsa,

  Chofunika n’kungomwetulira.