(Mateyu 9:37, 38)

 1. Yehovatu watipatsa

  zomwe timafunikira.

  Kuti tizisangalala

  pomwe tikum’tumikira.

  (KOLASI)

  Timadzipereka,

  pom’tumikira.

  Ndipo kulikonse tipita,

  mofunitsitsa.

 2. Padzikoli pali ntchito.

  Kosowa tidzapitako.

  Tikatero tisonyeza.

  kuti ena timakonda.

  (KOLASI)

  Timadzipereka,

  pom’tumikira.

  Ndipo kulikonse tipita,

  mofunitsitsa.

 3. Komwe tili kuli ntchito,

  inde, zofunika luso.

  Zinenero taphunzira.

  Ena tikulalikira.

  (KOLASI)

  Timadzipereka,

  pom’tumikira.

  Ndipo kulikonse tipita,

  mofunitsitsa.