Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Imbirani Yehova—Nyimbo Zatsopano

 Nyimbo 146

Munachitira Ine Amene

Munachitira Ine Amene

(Mateyu 25:34-40)

 1. Nkhosa zina zomwe Yesu ali nazo,

  zimatumikira ndi odzozedwa.

  Zomwe nkhosa zina

  zingawachitire

  Yesu adzawabwezeratu zonse.

  (KOLASI)

  “Mwakuwatonthoza, mwanditonthoza.

  Zonse zimene munawachitira

  munachitiranso ine amene.

  Zonse zomwe munawachitira.

  munachitiranso ine amene.”

 2. “Pamene ndinali wanjala, waludzu,

  munandithandiza mwamsanga ndithu.”

  “Mbuye, tinachita

  liti zimenezi?”

  Ndiyeno Mfumu idzayankha kuti:

  (KOLASI)

  “Mwakuwatonthoza, mwanditonthoza.

  Zonse zimene munawachitira

  munachitiranso ine amene.

  Zonse zomwe munawachitira.

  munachitiranso ine amene.”

 3. “Zabwino mwachita mokhulupirika,

  polalikira ndi abale anga.”

  Choncho mfumuyo

  idzauza nkhosazo:

  “Landirani dziko, moyo wangwiro.”

  (KOLASI)

  “Mwakuwatonthoza, mwanditonthoza.

  Zonse zimene munawachitira

  munachitiranso ine amene.

  Zonse zomwe munawachitira.

  munachitiranso ine amene.”