(1 Timoteyo 2:4)

 1. Timutsanzire Mulungu wathu

  Pokhala anthu opanda tsankho.

  Akufuna kuti anthu onse,

  Amve uthenga, apulumuke.

  (KOLASI)

  Wofunika ndi munthu,

  Osati mtundu wake.

  Tiphunzitse onse mosasankha

  Timakondatu anthu,

  Tiwauze uthenga

  ‘Akhale mabwenzi a Yehova.’

 2. Kulikonse angapezekeko,

  Kaya akuoneka motani,

  Mtima wawo ndiwo wofunika.

  Yehova amaona mtimawo.

  (KOLASI)

  Wofunika ndi munthu,

  Osati mtundu wake.

  Tiphunzitse onse mosasankha

  Timakondatu anthu,

  Tiwauze uthenga

  ‘Akhale mabwenzi a Yehova.’

 3. Yehova amalandira anthu

  Omwe asankha kum’tumikira.

  Choncho anthu a mitundu yonse,

  Tiwauze uthenga wabwino.

  (KOLASI)

  Wofunika ndi munthu,

  Osati mtundu wake.

  Tiphunzitse onse mosasankha

  Timakondatu anthu,

  Tiwauze uthenga

  ‘Akhale mabwenzi a Yehova.’