ONANI

(Chivumbulutso 7:9, 10)

 1. 1. Abale ambirimbiri,

  Inde ochuluka,

  Aliyense ndi mboni,

  Yokhulupirika.

  Tilipodi ambiri,

  Tikuchulukabe,

  Tachokeratu ku mafuko,

  Ndi mitundu yonse.

 2. 2. Abale ambirimbiri,

  Timalalikira

  Uthenga wabwinodi

  Kwa ofuna kumva.

  Ngakhale tingatope,

  Yesu atipatsa,

  Mpumulo ndi mphamvu zambiri;

  Tidzasangalala.

 3. 3. Abale ambirimbiri,

  Otetezedwadi,

  Otumikira M’lungu,

  Padziko lapansi.

  Tilipodi ambiri,

  Timalalikira,

  Timagwira ntchito ndi M’lungu,

  Pomutumikira.