ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Mateyu 4:4)

 1. 1. M’moyo wathu timafuna,

  Mawu a Mulungu.

  Azititsogoleratu;

  M’zonse timachita.

  Ndipo tidzasangalala,

  Ndi kudalitsidwa.

  (KOLASI)

  Chakudya chofunikadi;

  Ndi Mawu a M’lungu.

  Moyo wathu ufunika;

  Mawu a Mulungu.

 2. 2. M’mawuwo timawerenga

  Za anthu akale.

  Omwe anatumikira​—

  Mokhulupirika.

  Tikawerenga nkhanizi

  Zimalimbikitsa.

  (KOLASI)

  Chakudya chofunikadi;

  Ndi Mawu a M’lungu.

  Moyo wathu ufunika;

  Mawu a Mulungu.

 3.  3. Tikamawawerengatu,

  Tsiku lililonse.

  Tidzathadi kupirira,

  Mayesero onse.

  Ndiye tizikumbukira

  Zomwe tawerenga

  (KOLASI)

  Chakudya chofunikadi;

  Ndi Mawu a M’lungu.

  Moyo wathu ufunika;

  Mawu a Mulungu.