Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Imbirani Yehova Mosangalala

 NYIMBO 96

Buku la Mulungu Ndi Chuma

Sankhani Zoti Mumvetsere
Buku la Mulungu Ndi Chuma
ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Miyambo 2:1)

 1. 1. Pali buku limene mawu ake,

  Amatibweretsera chimwemwe.

  Mfundo zake zodabwitsa n’zamphamvu;

  Zimathandiza ’khungu kuona.

  Bukuli ndi Baibulo loyera.

  Olilemba anauziridwa,

  Ankakonda Yehova M’lungu wawo,

  Mzimu wake unawathandiza.

 2. 2. Analemba zokhudza chilengedwe,

  Mmene M’lungu anachilengera.

  Analembanso za Paradaiso

  Ndiponsotu mmene anathera.

  Analemba za mngelo winawake

  Amene ananyoza Yehova.

  Zinabweretsa chisoni pa anthu,

  Koma Yehova adzapambana.

 3.  3. Masiku ano tikusangalala

  Ufumu wa Mulungu wayamba.

  Yehova ’kupatsa chipulumutso

  Kwa onse omwe amamukonda.

  M’buku lake muli zosangalatsa;

  Chakudya chamwanaalirenji.

  Limatipatsa mtendere wambiri;

  N’lofunika kuliwerengadi.