ONANI

(Miyambo 4:18)

 1. 1. Aneneri akale ankafuna,

  Kudziwa za Yesu Mesiya.

  Mzimu wa M’lungu unaneneratu,

  Kuti adzatipulumutsa.

  Nthawi yakwana, akulamulira,

  Umboni wake ulipo.

  Kudziwa zimenezi ndi mwayi

  Waukulu womwe tili nawo.

  (KOLASI)

  Kuwala kwa panjira yathu;

  Kukuwonjezerekadi.

  Zomwe M’lungu akuulula;

  Zimatitsogoleradi.

 2. 2. Ambuye wathu wasankha kapolo,

  Ndi mmene amatidyetsera.

  Ndipo kuwala kwa cho’nadi pano

  Kukungowonjezerekabe.

  Pano tikuyenda molimba mtima,

  Mowala ngati masana.

  Tikuthokoza Yehova chifukwa,

  Cho’nadi chake watipatsa.

  (KOLASI)

  Kuwala kwa panjira yathu;

  Kukuwonjezerekadi.

  Zomwe M’lungu akuulula;

  Zimatitsogoleradi.