Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NYIMBO 91

Ntchito Yomwe Tagwira Chifukwa cha Chikondi

Sankhani Zoti Mumvetsere
Ntchito Yomwe Tagwira Chifukwa cha Chikondi
ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Salimo 127:1)

 1. 1. Yehova tikufuna;

  Kupemphera mokhudzidwa.

  Chifukwa mwatikonda,

  Ndipo tasangalala.

  Taona mwadalitsa,

  Ntchito imene tagwira.

  Ndipo tamangadi nyumbayi,

  Mwatithandiza.

  (KOLASI)

  Kukumangirani nyumbayi

  Yehova unali mwayi.

  Nthawi zonse tilemekeze dzina lanu

  Ndi kukutumikirani.

 2. 2. Mabwenzi achimwemwe,

  Taonani tawapeza.

  Sitidzaiwala mpakana

  M’moyo wosatha.

  Taona mzimu wanu,

  Mukugwirizana kwathu.

  Mwayi taupeza wokwezadi;

  Dzina lanu.

  (KOLASI)

  Kukumangirani nyumbayi

  Yehova unali mwayi.

  Nthawi zonse tilemekeze dzina lanu

  Ndi kukutumikirani.