ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Aheberi 10:24, 25)

 1. 1. Pomwe tikulimbikitsana

  Kutumikira Yehova,

  Chikondi chathu chimakula;

  Ndipo timagwirizana.

  Chikondi cha anthu a M’lungu

  N’chothandiza kupirira.

  Timatetezedwa kwambiri,

  Tikamakhala mumpingo.

 2. 2. Mawu a pa nthawi yabwino

  Amalimbikitsa ndithu.

  Mawu awa olimbikitsa

  Amachoka kwa abale.

  Kugwirira ntchito limodzi

  Kumatisangalatsadi.

  Tikhaletu olimbikitsa

  Ndiponso othandizana.

 3. 3. Pamene tsiku la Yehova

  Layandikira kwambiri,

  Tifunika tizisonkhana

  Kuti tiyende ndi M’lungu.

  Tigwirizane ndi abale

  Titumikire limodzi.

  Choncho timalimbikitsana

  Kuti tikhulupirike.