ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Salimo 25:4)

 1. 1. Yehova tasonkhanatu pamodzi,

  Pomvera kuitana kwanu.

  Mawu anu ndi nyale m’njira yathu,

  Amatiphunzitsa za inu.

  (KOLASI)

  Ndiphunzitseni njira zanuzo;

  Ndikhale womvera malamulo.

  Ndiyendetseni m’njira yoona,

  Malamulo anu ndizikonda.

 2. 2. Nzeru zanu Yehova ndi zakuya,

  Mfundo zanu n’zolimbikitsa.

  Mawu anu adzakhala kosatha,

  Timapezamo zodabwitsa.

  (KOLASI)

  Ndiphunzitseni njira zanuzo;

  Ndikhale womvera malamulo.

  Ndiyendetseni m’njira yoona,

  Malamulo anu ndizikonda.